chichewa   |   english

dziwani za ife

(about us)

Mbiri ya Chikhristu cha Stanley Black Phiri. Anaphunzira ma phunziro ake a ku pulayimale, ku sukulu ya Chilomoni L.E.A School, mu mzinda wa Blantyre, kuyambira mu chaka cha 1983, kufikira 1989, napita ku Chiradzulu Secondary School, kuchokako 1993.

Ndinapulumutsidwa monga wobadwa wa tsopano pomudziwa Yesu Khristu, kukhala Ambuye ndi mpulumutsi moyo wanga, pa 1 January 1993.

Phunziro la pa mtima ndi Geography. Ndinalembedwa ntchito ndi kampani ya "Peoples Trading Centre" mu chaka cha 1995, monga Imprest Clerk, ndinakwezedwa kukhala bulanchi manegala, mu chaka cha 1999.

Ndinatumikira Ambuye monga wotumikira pansi pa M'busa wa mkulu mu mpingo wa New Jerusalem Pentecostal Church, Jackson Frazer Mbewe kwa zaka zokwana zisanu ndi ziwiri 7.

Ndinadzodzedwa kukhala m'busa woima pa ndekha, mu chaka cha 2000, ku Area 23, mu mzinda wa Lilongwe.

Mu chaka cha 2008, ndinamvanso maitanidwe ena kukayambitsa mpingo wotchedwa "Full Life Pentecostal Church" m'Malawi, umene tinayambira kusonkhana mnumba ya m'modzi wa abale.

Ku chokera apa muchaka cha 2004, Ambuye analankhula nane za utumiki wa kupembedzera miyoyo ya anthu onse a padziko lapansi, ndi maiko amene kukuchitika nkhondo ndi zivomerezi.

Ambuye anandipatsa Mzimu wakuwawidwa,ndi miyoyo ya anthu ochuluka, okhala m'moyo wa chitaiko, ndipo nditapemphera kwa Ambuye anandivomereza kupita kukayambitsa utumiki wotchedwa "Out Reach Evangelistic Mission Ministry" kumene ndinadzala mipingo yokwana isanu ndi iwiri-7, kumalo akumidzi kutali ndi ntauni.

Mu chaka cha 2010-2011, ndinachita maphunziro anga a "Information Communication Technology", ku Ssukulu ya New Horizon, ndipo ndinakhonza mayeso anga a, International Diploma in Computer Engineering, ndipo ndinakhala Systems Administrator.

Ndinathandizanso anthu ochuluka powatumikira ndi kuwaphunzitsa, mautumiki osiyanasiyana, ndipo ena mwa iwo ndi azibusa m'mipingo yambiri, ena mwa iwo ndikutimikira nawo limodzi pakadali pano.

Ndimakonda miyoyo ya anthu ndi kukhudzidwa nayo,ndikuwapatsa chisamaliro. Odwala nthenda zosiyanasiyana, ndi onse ozunzika.

Ndimasamaliranso azibusa osiyasiyana, ena a pampingo wathu koma ena amipingo yosiyanasiyana, polipira nyumba zawo zimene amakhalamo.

Ndine wokonda mawu a Mulungu, ndikuyenda muchiyanjano ndi Mulungu kupyolera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu, kwa zaka zoposa 27, ndikuyenda ndi Mulungu.

Chokhumba change ndi choti ndichite mawu a Mulungu, ndi chifuniro chake nthawi ili yonse Iye akandifuna kukagwira ntchito yake.

Mukhonza kundipeza pa e-mail address yanga iyi hello@1way2god.info

tipezeni ife