chichewa   |   english

werengani izi

(read)

MONGA ANALI MASIKU A NOWA

(AS IN THE DAYS OF NOAH)

Nkhani ya Nowa ndi chigumula cha madzi ikupezeka m'bukhu la Genesesimutu 6 kufikira mutu 8, ndipo ikulongosola momwe dziko lonse la pansilinamizidwa ndi chigumula cha madzi, ndi momwenso Nowa pamodzi ndibanja lake anapulumukira mwa chisomo cha Mulungu, ndi pokhala nakokumvera pamaso pa Mulungu pomanga chombo chopulumukiramo. Pakuticholinga chenicheni cha phunziroli ndikufuna kuona gawo limodzi laGenesesi chaputala 6 chokha.

Genesesi mutu 6, kuyambira ndime yoyamba kulekeza ndime ya chinayi,(Genesesi 6: 1-4), ndi gawo lokondweretsa kwambiri kuwerenga. Ilolifotokoza motere: "Pamene mtundu wa anthu okhala pa dziko unayambakuchulukana, taonani pakuti ana akazi okoma m'maso anawabadwira iwo, kuti ana amuna a Mulungu anayang'ana akazi a anthu,kuti iwo analikongla, ndipo anadzitengera okhaakazi onse amene anawasankha. Ndipo anati Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthawi zonse,chifukwa iwonso ndiwo thupi la nyama, koma masiku ache adzakhala zakazana limodzi kudza makumi awiri. Pa dziko lapansi panali anthuakurukuru otchedwa a mtundu wa chi Nefilimu, ndipo pambuyo pake anaamuna a Mulungu atalowa kwa ana akazia anthu, ndipo anabalira iwo ana,amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omvekaMaumboni alipo ambirimbiri lero onena za anthu,amene ali abwinobwino,osati amisala ayi, koma oti anagwidwapo mokakamizidwa ndi anthuachiwembu, nkukawasunga kumalo akutchire(abducted), nawaumirizakuchita chigololo, mwina ndi m'modzi wa m'banja mwawo. Anthu ambirianyozapo maumboni a mtundu wotere, koma kukamba zoona zake zoterezizimachitika pamoyo wa munthu. Koma chomwe tingadziwe ndichakuti; zinthu zotere zolaulazi zomwe zikuchitika m'bado uno, muona kutisizinayambe lero kuchitika, koma kuti zinali kuchitikanso munthawi yaNowa, angelo amene anagwa pamodzi ndi satana m'mwamba, ndi ameneakufalitsa mbewu ya chilendo pakati pa anthu pophatikiza pamodzi mbewuya anthu ndi mbewu ya nyama za kuthengo.

Inutu mwina nkutheka kuti munamvapo pakuwerenga mabuku ofotokoza zambiri ya dziko la chi- Greek, yolongosola za uyo wotchedwa PEGASUS,yemwe ndi mbali imodzi munthu, mbali ina, ndi hachi, izitu zikhonzakukhala kuti ndi zoona ndithu. Muzaka za m'matwente (20) kumbuyoko,anzathu adza Sayansi padziko lapansi aphatikizapo mbewu ya munthu ndimbewu ya nyama nkuipanga kukhala khoswe kapena mbewa yomwe ili ndikhutu la munthu pambuyo pake. Chifukwa chomwe kafukufuku wotereyuwachitika,sichifukwa choti iwo akufuna chinthu chomwe chingathekumachiritsa nthenda zonse ayi, koma kuti mufufuze muona kuti izizimasonyeza machenjerero a m'dyerekeziyo, womwe akuumiriza(co-ersing),anzathu aza sayansi kuti azipanga zinthu zofuna kupikisanandi Mulungu,pofunanso okha kuziyesa ofanana ndi Mulungu mwa iwo okha. Awanso ndi mayesero ofanafana ndi mayesero amene satana anapereka kwaAdamu ndi mkazi wake Hava m'munda wa Edeni muja, choncho sizinthu zachilendo kuona ndi m'mene dziko la pansi lero lafikiramu. Munthawi yaNowa, angelo akugwa a satana aja, anali kusakaniza mbewu ndi mphamvuya mthupi yopangitsa kuti munthu pobadwa afanane ndi bambo omuberekakapenanso mayi omubereka imene tikuitchula kuti ndi ma. DNA, kuti ithekupanga cholengedwa chamtundu wake,monga tawerenga m'mabukhu achigiriki aja. Mwachitsanzo HERCULES anali chiphona ndi ochulukamphamvu, zotsalira za thupi lawo; monga mafupa amtundu wa anthu ngatiamenewa akhala akupezeka m'madera osiyanasiyana a dziko lapansilikufikira lero.

M'mapiri a Golani,ku Israeli kumapezeka mwala ozungulira omangidwapogwiritsa ntchito miyala ikuluikulu yomwe inapezeka kale kalem'mbuyomo, mbiri zikuti amodzi mwa ziphona munthawi ya Nowa amanyamulamiyala yotere namaiunjika pamodzi. Potengeranso kuti munthawi yakaleyokudalibe luso lapadera lonyamulira kapena kusuntha zinthu zolemerakuzichotsa malo ena kupita nazonso kumalo ena, koma mwa ichi, anthuamagwiritsa ntchito ziphonazo pofuna kusuntha miyala yolemera motere. Ndipo mbiri zoterezi ndi chitsimikizo choti mbiri za ngati izitikhonza kukhulupirira kuti zidali zoona. Ndipo dzina loti Nethilim limaperekedwa kwa ziphona zonga zimenetikuwerengazi, koma palitu maina ena m'malembo oyera atchulamonenetsa za chinthucho. Monga pamene ana a Israeli anakalowa mudzikola malonjezano lija,iwowa amayenera kugonjetsa ziphona mongatatchulazi, ndi kudzichotsa kotheratu. Munthawi yina pamene anaIsraeli anali kumeneko, tiwerenga nkhani ya Davide, mnyamatawachichepere oweta nkhosa za atate wake,yemwe adatumidwakukawabweretsera chakudya abale ake kunkhondo mbali zina za mdziko laIsraeli, adaona chiphona china chikuopseza ndi kunthunthumiritsaasilikali a Israeli, nayambana nacho chiphonacho kufikira anachidulamutu.

Dzina la chiphonacho ndi Goliati, dzina lomwe litanthauza kuti m'modziwa asanu. Mwachidziwikire adali ndi abale ake okwana anayi(4). Goliatiakuyenera kuti adali wamtali milingo 9 yausinkhu wake, mulingo womwesuli oyenera pa munthu wolengedwa bwino munthawi yomwe iyeadabadwayo. Zotsalira za mafupa zina zomwe zinkapezeka pa nthawiyozimakhala makamaka amuna zosachepera milingo makumi awiri kudzamphambu zisanu (25 feet tall). Anthuwa anali ooneka azitho ndi amphamvupamaso, koma osavuta kugonjetsedwa, chifukwa chamatupi awo ataliatali. Ndipo panthawi ya nkhondo akapezeka atagwa pansi zimakhalazovuta kuti adzukenso ndi kuyambira nkhondo ndikupambana. Anthuwa chomwenso amachita kunali kusakaniza mbewu ya angelo akugwandi mbewu ya anthu pamodzi ndi mbewu za nyama za kutchire, zimenezimakhala ndi kuthekera kosintha mbewu ya mthupi mwa munthu ndikuisokoneza, ndipo kena ndi kuipangitsa kukhala monga ziwanda. Cholinga cha zonsezi ndi kufuna kusokoneza ulosi umene unanenedwa kalendi aneneri a Mulungu kuti usakwaniritsidwe pa mtundu wa Ayuda. Muzigawo zambiri m'baibulomu tiwerenga mbiri ya ana a Israeli, kutiMulungu amawalamulira kuti aononge kotheratu mitundu ina ya anthu, izizili chonchi chifukwa mbewu ya mtundu wa ana a Israeli inasokonezedwandi machitidwe monga amene satana amalowetsa mbewu ya ziwanda mwa anaa Israeli, ndipo mitundu imeneyi sinali yochokera ku mbewu ya ana aMulungu komatu kumbewu ya satana mdiyerekezi, mitundu ina imene ana aIsraeli ankaiwononga motheratu yachirendo pamaso pa Mulungu. Ana aliwonse amene iwo amayenera kubereka ngati mtundu wa Israeli,umayenera kukhala mtundu umodzi wokha basi, choncho mitundu ina yonseimene ana a Israeli ankakumana nayo muchipululu muja amayenerakuiononga pamaso pawo kuti isapezekenso, kotero kopanda kuionongamitundu ya chikunjayo, kunalibe kupulumutsidwa kwa ana a Israeli,ndipo zinthu zawo pamodzi ndi miyoyo yawo ikadakhala yopandachiyembekezo pamaso pa Mulungu. Panali njira zambiri zomwe Mulunguakadatha kugwiritsa ntchito pofuna kuiononga mitundu ina ya anthu,koma njira imodzi yowoneka pamaso idali, kuti Mulungu anakhonzakubweretsa chigumula cha madzi monga munthawi ya Nowa, Iye adagwiritsantchito madzi apansi pano komanso madzi amthambo lakumwamba pofunakuononga mitundu ya anthu osamvera. Madzi apansi pano omwetimagwiritsa ntchitowa, ndiomwe tiwatcha Nyanja zathu za pansi pano,koma madzi amvula amene anagwa kuchokera kumwamba adali osiyanakwambiri pa nthawi ya chigumula cha Nowa chija. Anthu ambiriamakhulupirira kuti,ngati mvula yagwa ku dziko mochuluka kwa masikufote (40), singathe kudzadza dziko lonse lapansi pano, ikhonzakungodzadza mbali imodzi ya dziko, osati dziko lonse. Komabe, chimene anthu ochuluka amakhulupirira ndi choti, madzi womweamapezeka m'mwamba,mwa dziko lapansi amaphatikizana ndi madzi ameneamachokera m'Nyanja zikuluzikulu ndi m'mitsinje ina kudziko,ndi amenenthawi zonse amapanga mvula yomwe imagwa kuchokera kumwamba kudzeram'mitambo yomwe imabweretsa mvula, ndi omwe makamaka angathekudzadzitse dziko lapansili. Tikudziwa kuti chigumula cha Nowa chinalichokhudza dziko lonse la pansi pano, chifukwa anthu akhala akumapezazotsalira zina padziko lonse, kuyambira kuzigwa zing'ono zing'onokufikiranso m'malo mokwera a m'mapiri mudziko liri lonse, ndi maloena ambiri.

Kuli pulaneti imodzi yokha imene inatsala m'mwambamu, imeneinaphimbidwa ndi mulu wa madzi m'mwamba mwake, pulaneti imeneyitu,ngati sindikulakwitsa ndi yotchedwa kuti, VENUS. Apa tsopanotakhazikitsa umboni okwanira wonena kuti mvula ya chigumula cha Nowaija, inagwa dziko lonse lapansi, kudzera m'madzi amene anakuta dzikolonse lapansili. Mukhonza kufuna mutadziwa kuti,kodi chombo chimeneNowa anasema chidali chotani chomwenso chinatha kusunga banja la Nowa,ana ake amuna, ndi azikazi pamodzi ndi nyama zina zosawerengeka, zomwezinabwera pamaso pa Nowa kudzalowa mu chombo muja. Luso lapadera lojambula chithunzi chooneka mwaluso, kutengera ndi muutali,ndi mu lifupi mwake, monga ndi m'mene malembo oyera akunenera,ichitu chikadatha kukhala chombo chachikulu kwambiri m'masikuamenewo. Pulogalamu ya Kanema yakhala ikuulutsa kumanena kutichombocho chidali chozungulira, ili ndi bodza lalikulu. Kodi inumufuna umboni wa chombochi, m'mene chimaonekera? Zikomo kwambiri. Muzaka zoyambirira za m'ma 1950,ndege yina inajambula chithunzi chachombo pamwamba pa phiri lotchedwa Ararati, limene lipezeka kum'mawacha kumwera kwa dziko la TURKEY.

Koma patatha zaka zambiri, anthu ofufuzafufuza za mbiri ya zinthuzakale (Archaelogists), adapita kukayeza malowo, ndipo adapeza kutimuyeso wa chombocho umafanana kwambiri ndi muyeso umenenso baibulolidalemba. Pogwiritsa ntchito chida china chokwerera m'mwamba,atayezanso kuchokera pansi kufikira pamwamba pa chombocho, adapezakuti chidali ndi zigawo zitatu kuchokera m'musi mwake monganso baibulolikulongosolera kuti chombocho chidali ndi zigawo zitatu. Pochitakafukufuku wa mbiri ya midzi ndi mizinda yozungulira ikulongosoladzina la malo amene panali chombo cha Nowa mu chilankhulo cha chiTurkey amathandauza kuti ndi "Malo a Chombo".

Kenaka,pali mbili yolembedwa m'mabukhu yomwe idalembedwa ndi banjalina lake omwe adali mbali imodzi ya dziko lapansi mu zaka za ma 500 zapitazo, ikulongosola za nthawi yolondola ya chigumula cha Nowa. Awaanali, bambo,ndi mayi, ana awo amuna atatu pamodzi ndi akazi awo,monganso momwe baibulo likulongosolera pa nkhani imeneyi. Palibechikayikilo chili chonse choti ichi chidali ndithu chombo cha Nowa, ndikutinso, chigumula cha Nowa chidachitika monganso m'mene baibulolikulongosolera.

Munthawi ya chigumula cha Nowa, dziko lapansi linali lodzala ndichiwawa, ndi kusayera mtima kwa anthu, kudalinso kusakanizika kwambewu ya anthu, ndi mbewu ya angelo amene anagwa pamodzi ndi satana,mbewu ya m'magazi ndi yachilendo yomwe Mulungu sanayilenge mwa anthuake, cholinga cha zonsezi ndicho kuti satana amadzala mbewu zachilendo pakati pa anthu a Mulungu,pofuna kulisocheretsa dzikolapansi ndi machenjerero ake.

Pofuna kunena zoona palibe zinthu za mtundu wotere, cholinga chazonsezi ndi kufuna kupatutsa choonadi cha mbewu ya umulungu imene Iyemwini adadzala mwa anthu ake,ndipo satana akungofuna kupezerapo mwayiwofuna kusindikiza nambala ya 666 m'matupi mwa anthu makamaka pamphumi,kapena padzanja, kuti potero atipange ife kuti tisapulumukepamaso pa Mulungu. Iwo adzakuuzani kuti anapanga moyo wa munthu pansipano,ndipo wakhala akutiona ife kwa zaka za m'mamiliyonizapitazo,ndipo akufuna kutithandiza kukhala mwa mtendere pamodzi, ndikukhala anthu osagwidwa ndi matenda,ndikuti potero munthu akhonzansokukhala ndi zaka zochuluka monga zakanso za Adamu ndi abale ake. Chodabwitsa ndi chakuti kulumikizana ndi mizimu ya chilendoyi kwakhalakukuchitika zaka zochuluka, ndipo tsiku lina munthu adzaitana mizimuyoipayi, kuti izatithandize kukonza zinthu zomwe za sokonekera padzikolathuli. Nyengo zoipa, mphepo za mkuntho, kuphulika kwa ziphala zamotom'malo am'mapiri, kusefukira kwa madzi ndinso zivomezi zochitikaMadera osiyanasiyana a padzikoli,komanso ziwandazi zizakunamizani kutiAmbuye Yesu anatumidwa ndi izo, ndikunama kuti Iye si Mulungu koma ndim'modzi mwa milungu, ndipo ziwandazi zidza kunyengani ndi bodza lotiYesu,ndi Muhamadi,kapenanso mulungu wa Bhuda ali ofanana. Choncho ndifuna kukuchenjezani pano kuti ngati mukamvera bodza lasatanali, ndi kulikhulupirira ndiye kuti mukukhulupirira uthengawabodza, umene uli wosocheretsa anthu ochuluka, umene wapangidwa kutiusocheretse anthu ochuluka pansi pano,ndi cholinga choti inumuzitumikira atsogoleri awo kwa moyo wanu wonse, m'ngelo wotchukakwambiri wakugwa,ndi Lusifala,satana mwini. Pakuti iye ndi onseomtsatira kwaikidwa kwa iwo kuti malo awo ndi Nyanja ya moto, mongakwalembedwa m'bukhu la Chibvumbulutso,ndipo utsi wakuzunzika nawoukwera pamaso pawo nthawi zonse.

Komatu tsono ngati mukhulupirira chimene baibulo linena za Ambuyewathu Yesu, ndi chimene Iye wachichita pogonjetsa nkhondo ya satana, kupyolera mu mtanda pamaso pa zonsezi zazungulira dziko lathutikhalamoli,limene lamanga anthu ukapolo, anthu a Mulungu adzapulumukanakakhala naye pamodzi ndi Iye muulemerero wosatha m'mwambamo, choncho sipadzakhalanso ziphinjo zimene zakuta miyoyo ya anthu,chifukwa cha kusamvera Yesu ndi kukaniza choonadi cha Mulungu,nkumatsatira aneneri onyenga.

Mulungu amapereka moyo wolonjezedewawo, kukakhala opanda mabvuto,matenda,chisoni kapenanso imfa, koma tikhonza kuupeza moyo wosathakupyolera mu chikhulupiriro mwa Iye. Ngati Yesu Sali Mesiyawolonjezedwayo ndi Mulungu, munthawi yakaleyo, ndiye kuti ife amenetili okhulupirirafe, tidzakhala anthu amodzi omvetsa chisoni pamaso padziko lapansili, koma tsono zodabwitsa zimene Iye wazichita muzakazochuluka m'miyoyo ya anthu ndi nthawi yomwe Iye wakhala akuonekerakwa anthu, Iye wapangitsa amuna ndi akazi kukhala chimene lero Iye alipamaso pa Mulungu.

Yesu ameneyo ndiyemwe uja amene baibulo lakhala likunena za Iye, ndikunenanso kuti chipulumutso cha anthu sichipezekanso mwa wina ayi, komatu mwa Iye yekha, komanso sitingapeze chipulumutso popangantchito za bwino pokha ayi, komatu pokhala tili anthu omvera pamasopake, ndikunena kuti chipulumutso ndi mphatso yochokera kwa Mulungumwini wake kupita kwa iwo akukhala nacho chikhulupiriro mwa mwana wakeyekhayo khristu Yesu, tsono chaperekedwa kwa ife kupyolera pa kumveransembe ya Mulungu atate, tisakayendenso m'moyo womvetsa chisoni,dziko likapangidwa kukhala latsopano ndi lopanda matenda komanso imfa. Tidzakhala kunthawi zonse munyengo yonse ya mtunthu yakuchita bwinopamaso pa Mulungu, pamodzi ndi mulengi wathu yemwe anatuma KhristuYesu kudzatifera ife pa mtanda paja kuti tsono tikapulumutsidwekupyolera muimfa yake yopatulikayi. Pakuti tikhulupirira kuti yesuanawuka m'manda muja kutanthauza kuti nthchito yonse imene atate wakeadampatsa kuti ayigwire ikwaniritsidwe mwamtengo wapatali, ndikutitsono aliyense amene akakhulupirira imfa yake akayanjanitsidwe ndiAtate m'mwamba kudzera mwa Iye yekha Yesuyo, osatitu kudzera mwamphamvu zathu, kapena kuzindikira kwathu, koma kudzera muntchitoyaikulu imene Iye adaigwira pa mtanda paja.

M'bukhu la Mateyu 24 ndime ya 37 kufikira ndime ya 39, Yesu anatiuzazomwe ziyenera kuchitika,monga masiku womwe iye adzadzanso pansi panokudzatenga anthu ake. Monganso anali masiku a Nowa,choncho kudzakhalamonga kudza kwache kwa mwana wa munthu. Pakuti m'masiku a Nowachisanadze chigumula, anthu anali kudya ndi kumwa,kukwatiwa ndinsokukwatira, kufikira tsiku limene Nowa analowa m'chombo, ndipo iwosanadziwe kanthu kuti chichitike ndi chiyani kufikira chigumula chaNowa chinafika, ndikukokolola anthu onse. Umonso ndi momwezidzakhalire munthawi ya kudza kwake kwa mwana wa munthu.

Tangoonani ndi momwe ziliri zinthu m'masiku ano, anthu andale nawonsoakungokondera anthu ochepa, ndi kumasintha malamulo mokomera anthuoipa osapembedza Mulungu, ndi kusiya kuchita chifuniro chake chaMulungu, zinthu zomwe zinali zosavomerezeka mu zaka za m'ma 1960, panoanthu salankhulanso ndi pang'ono ponse angakhale zizilakwika. Mu zakaza m'ma 1960, ngati sindikulakwitsa mwina pothandauzila motsutsana ndimaganizo anu, komatu ngati simungathe kuvomerezana nane, ndiye kutiinu ndi munthu amene simufuna kugonjera kuchifuniro cha Mulungu.

Masiku alero ano ngati inu simungapezeke mukugwirizana ndi anthu pazinthu zolakwika zimene iwo akuzikhulupirira, ndiye kuti mudzakhalam'moyo wosalidwa ndi anthu adziko lapansili namanena kuti inu ndimunthu wopanda phindu pagulu la anthu, chifukwa mwa inu muli choonadicha Mulungu. Umunso ndi m'mene zinalili ndi Ambuye wathu Yesu Khristuanthu anthawi imene Iwo anali kuno ku dziko la pansili, anapezekakuti anasalidwa ndi anthu ochuluka,komanso kudedwa ndi anthu ambirichifukwa cholankhula choonadi pakati pa anthu, ndi chifukwa chakeananena mawu oti "Anandida opanda chifukwa", momwemonso dzikolapansili lidzakudani inu chifukwa cha Ine.

Ambuye Yesu anatichenjeza ife kunena kuti, pakuti anthu adziko linolapansi sanamulandire ndi kumuvomereza Yesu mwana waMulungu,chomwechonso dziko silingathe kuti vomereza ife ophunzira akeeni enife. Ku Briteni, kapena tinene kuti ku Mangalande(Britain),ngati utapezeka ukulankhula kuuza anthu kuti Yesu ndi njira yokhayoyokalowera kumwamba, angakhale utalankhula izi ukutumikira,kapenansokulankhula izi munjira ukuyenda, upezeka utatsutsidwa ndi anthuosavomereza,kuti Yesu ndi Ambuye, atayamba kukutsutsa, namakutengerakubwalo la milandu, kufikira atakulamula kulipira mulanduwo,pafupifupi 1000 pounds,ngati utalephera kulipira ukhonza kutumizidwakukagwira ntchito ya kundende, kalavula gaga. M'maiko ena apadzikolapansili,sungaloledwe ngakhale kuchititsa mapemphero a m'nyumbanzosatheka mpaka utamangidwa nazo.

Munthu wina wochenjera anayimitsidwa ndi apolisi limodzi mwa maiko akum'mawaku,ndikumfusa kuti amapita kuti. Podziwa kuti akadati alankhulezoona zake kuti akupita kumapemphero, a mawu a Mulungu ndiye kutipomwepo akadatha kumangidwa chifukwa chopita kukapemphera. Komatu Iyeanangonama kuti,mkulu wanga wamwalira ndiye tikukalongosola zamadongosolo ena,a zamalirowo,tikakumana usiku ukudzawu. Chonchomunthu wa poilisiyo anamulola kuti apitirize ulendo wake.

Mwachimwemwe tiyamika Mulungu. pamene mazunzo akubwera ana a Mulungu,akuchulukirachulukirabe,pa dziko la pansili,ifetu tikachita bwino moyouno,ndiye kuti sitidzakumana nawo,mabvutowo chifukwa cha mkwatuloulinkudzawo, kumene ana a Mulungu okhulupirira Mbuye wawo Yesuadzakakhala ndi Iye muyaya,masautsowa asanafike poipitsitsa. Ngatianthu anenetsa choonadi cha Khristu Yesu, osangotitu monga baibulolikufotokozera zonena kuti Yesu ndi njira ndi choonadi kokha ayi,komatu kulankhula kwa mtima wawo wonse ndi kutsimikizira bwino kutichimene achilankhula chili chochokera kuchikumbumtima chabwino, osatikunamizidwa ndi uthenga wina wa ngati wachoonadi,koma uli wa satanaayi, zimenezo.

Sizinafiketu pachimake penipeni, kuti tafikira uthenga kwa kuya,chifukwa anthu ochuluka adzagwa muchinyengo cha satana, zinthuzomwe Ambuye wathu adazilankhula kale lomwe kunena kuti m'msikuotsiriza anthu ambiri adzataya choonadi cha Mulungu nadzatsata njirazosokeretsa pamaso pa anthu. Ngati sitipemphera kolimbika kuti Mulunguafike powulula zinsinsi zake m'masiku ano otsirizawa, kuti anthuapulumutsidwe kuchokera kuchinyengo cha satanachi, ndiye ndi ndaniangathe kupulumuka payekha?

Ambuye akudalitseni pamene muwerenga chiphunzitsochi kawiri ndi kawiri. Ameni! Zikomo.

tipezeni ife