chichewa   |   english

werengani izi

(read)

MASOMPHENYA A MKATI MWA USIK? ZOCHITIKA M'MOYO WA KU GEHENA

(VISION IN THE NIGHT - ONE HELL OF AN EXPERIENCE)

Anthu ambiri afunsa funso; Kodi malo a Gahena wa moto alipodi, kapenamwina ndi zongokamba pansi pano? Kuchokera kuzinthu zomwe ine ndikuzidziwa, ndikhonza kulongosola wopanda kukaika kwina kulikonse, zamalo a Gahena wa moto, kuti ndi zoonadi Gahena alipod? Imanindifotokoze pa zomwe zinandichitikira mu chaka cha 199?Ndili mkati mwa pemphero, kupembezera anthu okhala munzindawachitayikowo, pamenepo ndinakhala Tsonga, ndipo ndinali ngatindatengedwa, mu uzimu, monganso Ezekieli analemba ndikuona gahenandi maso ak? Ambuye anali pamodzi ndi ine,nthawi yonseyi,ndi Ambuyeamene amandilimbikitsa ponditsogolera zoonekaz?

Mwina nkutheka kuti sizimveka bwino, kuti awa anali maso mphenya,koma kunena momveka bwino lomwe ndikhonza kunena kuti,izi zidalizochitika pa moyo wang? Ambuye anati kwa ine,kunena kuti sandisiyakukhala ndekha paulendo wonse umene ndimayendawo,munthawi yowonagahena wa moto? Koma kuti ndikazindikire kuti mukupezeka kwa Ambuyepakena kalikonse pa moyo wa munthu ndi kofunikira, koma kuti kwa onseamene adamwalira opanda Ambuye pa moyo wawo wa dziko lino la pansili,mphoto yake yaperekedwa kale kuti adzakhala mu gahene wa moto moyo waowons?

Nditafika ku malo aku gahena, chinthu choyamba kuchimva pa moyowanga, chinali kutentha kochititsa mantha kwa gahena wa motoyo,kotero mphamvu zinandichokera, koma kenaka ndinalimbikitsidwanso,nkutuluka ku malo oopsawa, motero ndinazindikira kuti sindikanathakuchita kanthu, pakuti sindinalinso,munthu wamthupi, koma wauzimu,koma kenekanso Ambuye anandithandizira kuti umunthu wanga wonseubwerere m'malo mwak?

Zitatha izi ndinali ndi chikumbu mtima cha anthu onse ameneamandiunikira za uthenga wa bwino m'misewu yambiri yomwe inendimayendamo,uthenga onena za chipulumutso cha moyo wanga, enaamachita kukandiikira mu bokosi nambala yanga ya ku positi ofesi, ndicholinga choti uthenga wa Mulungu undifikire ndikundipulumutsa, popezanthawi yomwe uli bwino lomwe opnda vuto,sulingalirapo za moyo wakokuti mwina ndikhonza kumwalira pa ngozi ya pansewu, kapena kutikudwalatu matenda kumene, zonsezi sindinazilingalire pa moyowanga,ndinkangoona ngati kuti nthawi ndi yochuluka pa moyo wanga wakuno kudziko la pansil?

Ndiponso kenaka ndinakumbukiranso ndi momwe anthu ena amathakundikhumudwitsa kwambiri pofikira kundipsetsa mtima, ngati ndi wabwenzere za chipongwe, koma ndi makanika kuter? Chifukwanso nanendimathanso kulingalira mwa kuya kuti ndimathanso kulakwira anthu enamonganso ena amandilakwira, nthawi zinanso ndimawalakwira mwadala,nthawi zinanso mwangoz?

Kenaka malingaliro amabwera ofuna kuwachenjeza achibale anga, zakuopsa kwa malo amoto wa gahen? Panalibe kanthu kuti mwina pali zinazimene ndi mazikonda, pa moyo wanga zomwe mwina sindingafune kuti ndizisiye kuzichita, komatu zinali zowawa kuzindikira kuti ndi koopsakwambiri kuti ndine wosakhululukidwa moyo wanga wons?Koma tsono chinthu choipitsitsa pa zonse ndi kuzindikira kuti, Mulunguadandinyanyala moyo wanga wonse, ndi kutinso ndilibe chiyembekezochina chili chonse, moyo wanga wonse kuchokera kumazunzo a moto wagahen?Ndipo kenako Mulungu ananditenganso ine, nandibwezeretsamwakale, koma chondilimbikitsa ndi chakuti ndinali munthu wosinthikakwambiri chifukwa cha zomwe ndinazionazoTsopano ndinadziwa zina zochepa za zomwe zikawaonekera anthu onseokhala moyo wa chitayiko pansi pano, kuti azasiyidwa ndi Mulungu,kutsutsidwa kwa moyo wosatha kopandanso kuti mwina mwayi ungazapezekewoti nkulapa machim? Nditatha kuona izi, nthawi ina ili yonsendikamapempherera anthu otayika,kuti apulumuke, inetu ndimapempherandi misonzi m'maso mwanga, chifukwa ndinaona zinthu zoopsa zimenezikudikira anthu osapulumutsidwa ndi Khristu Yesu,ngati iwo sabwerakwa Ambuye Yesu asanamwalir?

Tsopano ndidzachita china chilichonse, kupita kwina kulikonse, mudziko ili kukachitira umboni, za momwe Ambuye ayendera modabwitsa pamoyo wanga, ndi kulongosoleranso anthu ena momwe tingapewere gahena wamoto kuti tisakalowem? Tiyamika Ambuye Yesu, pochita china chilichonse chofunikira, powonetsetsa kuti pasakhale munthu ndi m'modziyemwe wopita ku gahena wa moto, kupatulapo chinthu chimodzi, Iyewatipatsa mwayi wonse wa ntunthu kupanga chisankho chogwiritsa ntchitozomwe Iye watiuza kuti timvere, kapena kukana ndi kusamvera zomwe Iyewatiuz?

Ngati timuvomereza Iye m'moyo uno wa dziko la pansili, ndikuyendamuchiyanjano ndi Iye, dziwani kuti tidzakhala naye kwa muyaya moyowathu wons? Ngatit inu mupita kugahena, ndiye kuti zikungowonetserapoyera kuti simunapange chisankho chomulandira Ambuye wathu Yesu,kukhala Ambuye ndi mpulumutsi wanu, Ambuye ndi bwenzi lanu,ndikupempheni kuti mumulandire Ambuye Yesu kukhala Ambuye ndimpulumutsi wa miyoyo yanu nthawi isanath?

Inu abale ndi alongo mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, ndikupemphani kutimukhale nako kuthekera kokhonza kuchita china chili chonse, pofunakubweretsa miyoyo yochuluka imene ndi yotayika kwa Ambuye wathu Yes?Anthu mdziko lino ambiri akufatu mkati mwa usiku uno, asanamve mawundi uthenga wa moyo wa Yesu Khristu,?(Chipulumutso kudzera mu nkulapandi muchiyanjano ndi Yesu Khristu, osatitu kupyolera muntchito zabwino ayi), tiyeni tingoganiza kuti ngati ife sitiwafikira anthuotayikawa,ndiye ndi ndani angawafikire iwo? Ambuye akudalitsen? Zikomo!

tipezeni ife