chichewa   |   english

werengani izi

(read)

NDINGATANI KUTI NDIPULUMUTSIDWE?

(WHAT MUST I DO TO BE SAVED?)

Ili ndi funso limene anthu ochuluka anali kufunsa mu nthawi ya Ambuye Yesu pamene anali pa dziko la pansili, yankho limene amalipeza limakhala lalifupi kwambiri koma lokhala ndi mfundo zomveka bwino. Mu bukhu la Machitidwe chaputala cha 2:37-39, mtumwi PETRO anafotokoza motere:" Tsopano iwo atamva izi analaswa m'mitima mwawo, ndi kuti, kwa PETRO pamodzi ndi atumwi enawo, amuna inu ndi abale, tingatani ife kuti tipulumuke?"

Ndipo PETRO anati kwa iwo, "Lapani ndi kubatizidwa aliyense wa inu mu dzinala la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuloza ku chikhululukiro cha machimo ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu woyera, pakuti lonjezo liri kwa inu ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akukhala kutali, angakhale iwo ochuluka amene adzayitanira pa Ambuye Mulungu wawo". Chikhululukiro makamaka chichitike ndipo chikhale choona.Mawu awa akutanthauza kuleka njira zoipa ndi kutsata njira za chilungamo.

Izitu zitanthauza kuleka kuyenda moyo wosangalatsa iwe mwini ndi kutembenukira kuyenda moyo okhawo okondweretsa mulungu, kuphatikizapo kuyenda moyo wa chiyero pamaso pa Mulungu tsiku ndi tsiku. Ngati muli nako kuthekera kuthupi kokhonza kuthandiza anthu ena , ndiye kuti zili bwino kwambiri, komatu tsono iziz zimathangatiridwa ndi moyo wa chiyero womwe umakondweretsa Mulungu nthawi zonse.Anthu ambiri sanamve za uthenga wa bwino wa Mulungu, uthenga wa bwino wa Ambuye Yesu, choncho uthengawu uli wa anthu amene sanamudziwe Ambuye komanso anthu amene angomudziwa kumene Ambuye.

Mu bukhu la YOHANE chaputala cha 10:28-30, mtumwi PETRO akulemba zinthu zomwe anazimva Yesu akulankhula, "NKHOSA ZANGA ZIMVA MAWU ANGA, NDIPO NDIZIDZIWA KOMANSO ZINDITSA INE, ndimadzipatsa moyo wosatha ndipo sizidzaonongeka, ndipo pali wina angazichotse mdzanja mwanga. Atate wanga amene anandipatsa, ali wa mkulu kuposera izo, ndipo palibe munthu amene angadzichotse mdzanja la Atate wanga, pakuti Ine ndi Atate ndife amodzi.

Apa mukhonza kuona nokha kuti pamene muyitana Ambuye Yesu mu mtima mwanu, ndi mtima otsegula tsono ndi udindo wake wa Ambuye Yesu kutsiriza ntchito ya chipulumutso cha moyo wanu Ambuye Yesu asanabwere kudzaweruza anthu pa dziko la pansi li. Pakuti anthu apa dziko ili la pansi adzakhala ndi chiweruzo cha mitundu iwiri, choyamba ntchito zimene iwo agwira zidzaunikidwa mokwanira, chomwecho za bwino ndi zoipa zonse zidzaunikidwa.

Kachiwiri iwo adzaweruzidwa molingana ndi m'mene analandirira uthenga wa bwino wa Yesu Khristu, ngati iwo anamulandira Iye monga Mpulumutsi, Mesiya ndi Ambuye adzalandira mphoto ya ntchito zawo mu ufumu wa Mulungu m'mwamba. Tsono tiyeni tione zomwe Ambuye Yesu analankhula za iwo anakhulupirira mawu ake mu nthawi ya moyo wawo pansi pano, Iye asanabwere kudzkwatula oyera onse, ndi amene ali oyenera kuthawa chisautso chachikulu chili mkudza pa dziko lonse la pansi, ndikutengedwa mu mkwatulo uli mnkudzawu.

YOHANE chaputala cha 5:24, akufotokoza bwino momveka, kuti iye akhulupirira Ine sadzaweruzidwa koma waoloka kale kuchokera ku imfa ndi kulowa ku moyo wosatha.Zingathe kukhala zovuta kuti tikaweruzidwe, osayangana ntchito zathu zimene tagwira pansi pano. Aefeso chaputala cha 2:8-10, akufotokoza momveka bwino, pakuti ndi Chisomo cha Mulungu kuti inu mwapulumuka, kudzera mu chikhulupiriro osati mu ntchito zanu, koma ndi mphatso yake ya mulungu kuti inu mupulumuke. Simonga mwa ntchito kuti mwapulumuka koma ndi chisomo cha Mulungu .Pakuti ife ndi chimango cha Mulungu, wolengedwa mwa Khristu Yesu kuti kukachita ntchito za bwino, zimene Mulungu anakonzeratu lisanakhale dziko la pansili. Kuchita kwathu kothangatira chipulumutso ndikosakwanira, kuti tikhonza kudzipulumutsa tokha. Bukhu la YOHANE chaputala cha 20:28-30, tiwerenga mawu otsiriza amene Ambuye Yesu analankhula, "Iye anati tsopano kwatha!".Ndipo anagwetsa mutu wake pansi, napereka mzimu wake kwa Mulungu Atate, ngati chinthu chatsirizika ndiye kuti chatha, palibenso chimene chatsalapo. Pamene Iye anafa pa mtanda paja ndiye kuti anali atatsiriza ntchito yonse imene Atate wake anamutuma kudzagwira pansi pano, kupanga njira ya tsopano yoti munthu lero atsate pokafika ku mpando wa chifumu wa Mulungu ndikuti Iye anapanga kuti pakati pa munthu ndi Mulungu pakhale chiyanjano chomwe chinalipo m'munda muja mwa EDENI.

Chomwe chikungofunika pano ndi kukhulupirira uthenga wa bwino wa Ambuye Yesu Khristu, ndikuyesetsa kukhala moyo woyenera mayitanidwe amene Mulungu anachita pa ife pokhala mu chiyanjano ndi Mulungu cha tsiku ndi tsiku. Pamene Ambuye Yesu anauka m'manda muja anaonetsera ku dziko lonse kuti Iye anali amene wakhala akunena za Iye mwini kuti ali mwana wa Mulungu, ndi mwini moyo, munthu wapadera dera wokhala ndi maonekedwe a Mulungu ndi a munthu, ali pansi pano Iye anapanga zinthu zonse zimene anthu amachita pansi pano.

Zonse zimene anapanga Ambuye Yesu kunali kuonetsera kuti, si munthu amene anafunafuna Mulungu, koma Mulungu anatumiza mwana wake kuti akafunefune munthu wotayika kuti adzenso pamaso pake ndi kuyanjana ndi munthu. Ambuye Yesu ndi okhawo amene anakwalitsa kusunga pangano osangoti kokha kuti machimo a munthu akhululukiridwe, komanso kuti munthu akakhonze kukhala ndi moyo wosatha wa muyaya.

Chipangano chimene Mulungu anapangana ndi anthu a nthawi ya MOSE, chinali choti mwana wa nkhosa adziphedwa m'malo mwa munthu wochimwa, kotero kuti munthu wochimwayu abwererenso m, manja mwa Mulungu amene amadana nalo tchimo. Yesu ndi amene anali, ndipo ali, wopangitsa kuti munthu wochimwa ayanjanenso ndi Mulungu kawiri, pakufera zochimwa zathu, kuyambira kale, panopa, ngakhalenso mtsogolomo, palibenso wina, kapena Angelo, kaya ziwanda, kaya ndi maukulu ndi maulamuliro aza mdima uno, angathe kusintha chili chonse chimene Ambuye Yesu anatichitira ife, anatipulumutsa kwa mtunthu palibe wosintha zimenezi.

Pemene munthu anakodwa ndi tchimo ndikuti munthu anazipanga yekha kukhala mulendo pamaso pa Mulungu, Yesu anabwera kudzatipulumutsa choncho kuti ife tipange chisankho chomutsata Iye ndikuti tikhale ndi moyo wosatha, kapena kusankha njira ya uchimo kuti tikakhale anthu opanda chiyembekezo cha moyo wosatha. Ambuye Yesu sakufuna anthu opangiridwa zochita, kapena kukakamizidwa popanga zinthuayi, koma anthu okhawo angamukonde Iye ndi mtima wao wonse, kukakhala naye mu ufumu wa Mulungu kwa muyaya. Iye ndi mwana wa Mulungu ndi mpulumutsi wa dziko lonse la pansi.

Taonani pano chinthu chatsopano chimene Ambuye Yesu achichita mu nthawi ya masiku ano. Zaka zambiri zapitazo kunali mtsutso pakati pa anthu, ndipo izi zinadzetsa zipolowe kufikira anthu ena anatengeredwa ku bwalo la milandu. Ndipo oweruza mulandu analamulira kuti munthu amene anatsogolera zipolowezo, atsekeredwe kufikira atalipira ndalama pa mulandu umene analakwawo. Koma munthu wina wake atamva izi anatenga ndalama nalipira mulanduwo m'malo mwa mtsogoleri woyambitsa zipolowe uja, ndipo monga mwa lamulo, munthu oweruza mulandu uja anayenera kumvomera kutulutsa munthu uja, ndipo kuyimbidwa kwa mulandu kwa munthu wolakwa uja kumathera pomwepo.

Zimenezi zikusonyeza kuti Ambuye Yesu anaima m'malo mwa ife tonse pamene anali kupachikidwa pa mtanda paja ndiye kuti anali kulipira mulandu wa ife tonse anthu ochimwa. Apa tili ndi mwayi wopanga chisankho chomvomereza kuti Ambuye Yesu analipira mulandu wathu, ndi kuti ife tonse tipulumuke ku chilango cha imfa, kapena apo ayi kulandira chilango cha zotsatira zake za machimo athu. Kupulumutsidwa kutanthauza kuti ife timvomereze ndi kukhulupirira zonse zimene zalembedwa m'bukhu loyera, ndi kukondwera. Chipulumutso chanu sichidalira pa inuyo, koma kwa mtunthu Ambuye yesu pakuti Iye ali okhulupirika, mdani wathu satana sangathe kutikwatulanso mdzanja la Ambuye wathu Yesu, koma ndinu otetezeka mdzanja lake kwa muyaya, odalitsika akhale Mulungu Atate wa m'mwambamwamba. Chitsimikizo chakuti Mulungu anamvomereza kuti Yesu akhale nsembe ya chipulumutso chathu, ndi chakuti, Iye Ambuye Yesu anaukitsidwanso m'manda muja atafa natha masiku atatu ali m'manda, chiyanjano chamtundu wotere chidzakhala ku nthawi ya muyaya. Ameni!

tipezeni ife