chichewa   |   english

werengani izi

(read)

MWASANKHA YESU CHIFUKWA CHANI?

(WHY CHOOSE JESUS?)

KUSIYANA PA MAONEKEDWE A CHIKHRISTU. (The Uniqueness of Christianity)

Ku dziko la pansili kuli zipembedzo zosiyanasiyana,ndipo kuti munthu aliyense ali nawo ufulu osankha chipembedzo cha pa mtima pake. Chiphunzitso chimene chalembedwachi sichikutanthauza kuti tikufuna tidzudzule munthu wina aliyense ,maka tikamayangana zinthu zokhudzana ndi chikhristu, zomwe zikusiyanitsa . Chomodzi mwa zikhulupiriro ndi chakuti ,ambiri amakhulupirira kuti Mulungu anatsika pansi pano,ka nthawi kochepa kudzakhala ndi anthu omwe Iye anawalenga,ndikuwaonetsera njira ya bwino yoti azikhulupirira Mulungu kamba ka ulemerero wa Mulungu Atate.

Chimodzi mwa zinthu zomwe zinagwedeza mitima ya anthu mu nthawi yomwe Ambuye wathu Yesu Khristu anakhala moyo wa pa dziko lino la pansi, ndi chakuti, Iye mwini anali kumutchula Mulungu kuti Atate wake,amene ndithu ali Atate wake.Mulungu yemweyo anali ndipo wa mphamvu zonse ,anasiya dziko lokoma la ku mwamba lodzala ndi ulemerero,pa kanthawi komwe anangosiya ndi kuvula ulemerero wa kumwamba, ndi kudzakhala pansi pano,monga munthu wina aliyense amakhala. Koma kusiyana kwake kuli poti Ambuye wathu Yesu sanakhale moyo wa uchimo pansi pano.

Zipembedzo zina zambiri zimanena kuti mulungu wao alibe mwana,koma Akhristu amakhulupirira kuti,Ambuye yesu ndi mwana wa Mulungu,chifuka chamalembo oyera amene analembedwa ndi iwo amene anali pamodzi ndi Iye,mu nthawi yomwe Ambuye Yesu anali kuno ku dziko la pansili mu zaka zokwana 30. Modzi mwa anthu ena analemba za kubadwa kwacha,monga; "Koma atatha kulingalira mokwanira za izi,taonani mngelo wa Ambuye anamuonekera iye nati,ku maloto, YOSEFE iwe mwana wa Davide,usakhale ndi mantha kudzitengera wekha MARIYA, mkazi wako,chifukwa kuima kumene waima mkazi wako ndi kochokera kwa MZIMU WOYERA.

Pakuti Iye adzabala mwana wa mwamuna,ndipo udzamucha Iye kuti,YESU,pakuti adzapulumutsa anthu ake ku machimo. Ndipo zinthu zonsezi zinachitika kuti chikakwaniritsidwe chonenera cha Ambuye Mulungu Atate kupyolera mwa ANENERI awo. "Taonani mnamwali adzayima nakhala ndi pakati nadzabala mwana wa mwamuna,ndipo iwo adzamucha Iye EMMANUELI, dzina lomwe litanthauza kuti ,MULUNGU ALINAFE, (GOD WITH US).

Anthu omwe amatsatira bwino za kafukufuku wa mbiri za kale,(MYTHOLOGY),amadziwa kuti pamakhalanso, kubadwitsa kwa mtsikana wa chichepere zoterezi,ngakhale zoterezi zimakhala kwambiri ana a akazi,kudzera mukusowa kwa mbewu yomwe imathandizira kubereka,mwana (CHROMOSOME), koma kubadwa kwa Ambuye Yesu sikunali kotero,kunali kosiyaniratu ndi mabadwidwe a anthu ena onse a pa dziko lino la pansi,chifukwa mwa njira ngati yomweyi yopanda mbewu ya mwamuna, koma Ambuye Yesu anabadwa nakhala mwana wa mwamuna.Ambuye Yesu ndipo anawakonda anthu womwe Iye anawalenga,kotero anafunitsitsa kuti abwere nakhale nawo pamodzi kuno ku dziko la pansi,monga munthu amene anadzipereka yekha kufa pa mtanda,ndikulandira chilango choyenera anthu kuti akaphedwe ndipo chinamugwera Iye yekha,ndikupanga njira yoti munthu abwererenso kwa Atate Mulungu ,ndikupanga chiyanjano ndi Mulungu,chiyanjano chimene Adamu ndi Hava anachitaya m'munda muja poswa pangano ndi Mulungu.

Mwatsoka lake anthu ochuluka samakhulupirira nkhani ya Adamu ndi Hava,chifukwa imafotokoza za kuyesedwa kwa ndi NJOKA (SNAKE OR SERPENT). Chimene anthu samazindikira ndi chakuti,liwu loti NJOKA (SERPENT),limafotokozera za MDIYEREKEZI,osati makonzedwe ake akuthupi kapena maonekedwe. Mwachidule,tinene kuti m'bukhu la LUKA chaputala cha 13:31 -34, Ambuye Yesu anauzidwa kuti Herodi akubwera kudzamugwira ndi kuti athawe,koma apa tikuona Ambuye yesu akuyankha motere: Ndipo tsiku lomwelo taonani kunabwera a Farisee ena ,nati kwa Iye," chokani inu kuno ,chifukwa HERODI afuna kupha inu", ndipo Ambuye Yesu anati kwa Iwo, "mukani kayiuzeni NKHANDWEYO (FOX), taonani, ndili kutulutsa ziwanda, ndipo ndi chilitsa anthu lero,ndi mawa,ndipo tsiku lachitatulo,ndidzalungamitsidwa. Taonani pakuti sikuyenera kuti mneneri akafere kunja kwa mudzi.

Apa sanali kutanthauza kwa ka nthawi kuti,HERODI anali ndi tsitsi lofiira ayi,kuonjezera apo, mu bukhu la 2 Akorinto chaputala cha 11:14,mtumwi PAULO akulemba kuti, "Ndizosadabwitsa,kuona satana mwini akudzikhalitsa maonekedwe angati a mngelo wa kuunika." Dzina loti satana ndi lomwe anthu ambiri akhala akutchulira mdani wathu,wa mkulu,yemwenso ndi mdani wa Mulungu ndi mdani wa zinthu zonse za bwino,amene ali mwini wa uchimo mdziko la pansi.

Chimodzi mwa zinthu zomwe zili zosiyanitsidwa pa chikhristu,ndi nkhani ya chipulumutso,kumasulidwa ku mphamvu yoipa ,ndipo chikondwerero cholungama, chili pa akhristu ,ngatitu mutakhala kuti mukuyenda moyo wa chiyero ndi kuti mwafa muli olungama, mudzalandira chipulumutso monga mphatso ya pa kuchita bwino,pamaso pa Mulungu . tangoganizani kuwawa kwake ndi kotani koti munthu wakhala wa bwino,kukhalanso wachifundo kwa anthu ena,kuthandiza anthu osowa,kudyetsa anthu anjala ,kumwetsa anthu aludzu ndi kuwapatsa,pogona anthu osowa malo,ndipo kenako ndi kukapezeka kugahena,zonse zija kukhala za chabe chabe.

Ndiponso mtumwi PAULO anafotokoza bwino lomwe mu bukhu la AEFESO chaputala cha 2:8-10:" Pakuti mwa chisomo inu munapulumutsidwa,osati chifukwa cha inu nokha,ndi mphatso ya Mulungu,osati chifukwa cha ntchito,kuti wina angathe kudzitamandira. "Pakuti ife tili opangidwa ndi Iye, wolengedwa mwa Khristu Yesu,ku ntchito ya bwino, wokonzedweratu ndi Mulungu dziko lisanati,kuti tikayende pamaso pa Mulungu.

Mu bukhu la MATEYU,chaputala cha 7:21-23,apa tikuona Ambuye Yesu akulankhula za tsiku lomaliza la chiweruziro,kumene munthu wina aliyense adzadza ku mpando wa chiweruzo,wa Mulungu,posatengera kulakwa kwawo,kapenanso kuchimwa kwawo. Ndipo ambiri pa nthawiyo adzabwera kwa Ine nanena kuti, Ambuye ,kodi ife sitinachiritsa odwala mu dzina lanu,kutulutsa ziwanda mu dzina lanu,ndi kuchita ntchito zambiri za bwino ?.Ndipo Ambuye Yesu sikuti akukana zonsezi,koma adzati ,chokani kwa Ine ,inu anthu ochita kusaweruzika, chifukwa choti anthu ambiri sanakhonza kuyenda ndi Ambuye Yesu moyo wawo wa tsiku ndi tsiku.

Ntchito za bwino zimayenera kutuluka pamaso pa Mulungu pamene anthu ali mu chiyero ndi Mulungu,ndipo mphoto zimayenera kutsatapo,osati monga mwa ntchito zawo zomwe anazipanga ponofuna kulandira mphoto chabe. Anthu ambiri amapanga zinthu za bwino ndithu kuti akangoyandikirana ndi Mulungu. Tingathenso kuona kuti kuyambira mu bukhu la GENESESI chaputala cha 15:1-6, kumene Mulungu ali kupanga mapangano ndi ABRAHAMU.

Ndipo patapita izi,taonani mawu a Mulungu anadza kwa ABRAHAMU,mu masomphenya:

"Usaope ABRAHAMU, ndine chikopa chokunjiriza iwe,mphoto yako yaikulukulu". Koma ABRAHAMU, anati Ambuye Mulungu wamkulu Inu,kodi muzandipatsa ine chiyani,pakuti ndine munthu wosowa mwana ,ndipo kodi amene mwandipasa wa ntchitoyu ndiye wotenga chuma changa, ELIEZER,wa ku DAMASIKO? Ndipo ABRAHAMU, anati, "simunandipatsa ine ana; choncho wa ntchito wa mnyumba mwanga ndiye adzakhala wolamulira chuma changa ?. Ndipo taonani liwu la Mulungu linadza kwa iye,"Munthu uyu sadzakhala olowa ndi kulandira chuma chako,monga mbewu yako ayi,koma mwana wako wa iwe wekha wobadwa kuchokera mu thupi lako,ndi magazi ako ndiye adzakhale wolowa mnyumba mwako ndikukhala wolandira chuma chako. Pamenepa ndipo Yehova Mulungu anamtenga ABRAHAMU namuka naye kunja kwa nyumba, ndipo YEHOVA anati kwa iye, yang'ana kumwamba,ndipo werenga nyenyezi za kumwamba,ngatidi ungather iwe kuziwerenga izo". Ndipo anati kwa iye ,momwemo zidzakhala mbewu zako.

Ndipo pamenepa ABRAHAMU anakhulupirira YEHOVA Mulungu, ndipo kwa iye kunayesedwa kuti anali wolungama. Zoterezinso,zikungofuna kufotokoza mtundu wa paderadera wa Chikhristu chathu kuti chiyenera kukhala chosiyaniratu,ndi anthu ena onse. Kumakhulupirira zinthu zomwe Ambuye Yesu akuphunzitsa,komanso zinthu zomwe baibulo likufotokoza ndi kuyamba kuyenda pamaso pa Mulungu tsiku ndi tsiku,basi izi ndi zomwe inu muyenera kumachita,pofuna kukakhala moyo wanu wonse ndi Ambuye Khristu Yesu mu ufumu wake,komanso kukakhala pamodzi ndi Mulungu wolenga zinthu zonse zooneka ndi maso komanso zosaonekazo.

Chinthu china mwa zinthu zomwe zingapangitse kuti chikhristu chikhale chinthu chosiyanitsidwa pa zinthu zonse ku dziko la pansi,ndicho kuti," Tikhale ndi chikhulupiriro chachikulu pomvomereza kuti Ambuye Yesu anafa pa mtanda ndipo anauka m'manda muja,atatha kuyika pangano ndi anthu onse a ku dziko la pansi kusenza machimo awo onse,pa mtanda, kuyambira nthawi za kale, nthawi zatsopano,komanso nthawi za kutsogolo,kotero kuti munthu wina aliyense amene angathe kukhulupirira mwa Iye, kuti Iye ali ndani,komanso kuti Ambuye Yesu anachita zinthu zambiri zosawerengeka populumutsa anthu anthu amitundu yonse,kuyambira amuna ,azimayi,ndiponso ana omwe, kudziko la pansi kupyolera pa mtanda wa pa KALIVARE (Calvery),kufikira nthawi ya chimaliziro cha pansi pano. Ngatitu mudzakhulupirira zimenezi ndiye kuti moyo wanu udzasinthika ndi kuchita bwino.

Pomalizira,"kodi pali umboni lero masiku ano otsirizira,osonyeza kuti Ambuye Yesu alipo ndipo ali ndi moyo,ndipo kuti akhonza kuthandiza iwo onse akuyitanira pa dzina lake,kodi kapenatu kwa anthu ena nkhani za Yesu Khristu zilingati nthano chabe?.(myth?), Pofuna kuyankha funso la mtundu wotere, choyamba mudziyang'ane kaye nokha,ndiukuyang'ana kumene mwachokera,komanso kuona anthu ena amene anali zigawenga zakupha anthu,anthu akuba,oledzera,odzadzidwa ndi zinthu zochuluka zonyasa,koma kuti tsono lero ali kuyenda ali angwiro pamodzi ndi Ambuye Yesu omwe anasinthika chifukwa cha mawu ake a YESU.Ili ndi gawo limodzi mwa magawo a zinthu zooneka ndi maso kuti Ambuye Yesu anuka m'manda muja kuchokera kwa akufa, mwa umboni winanso werengani,nkhani imene ili m'munsiyo:

ZOONA ZAKE ZENI ZENI ZA NSALU YOMWE ANAFUNDITSIRA THUPI LA AMBUYE YESU M'MANDA MUJA-YOMWE INAKAPEZEKA MU MZINDA WA TURIN MDZIKO LA ITALY.(The Truth about Turin Shroud).

Kwa zaka zochuluka tsopano pakhala pali mtsutso waukulu pakati pa anthu ochuluka pa nkhani ya nsalu yomwe anafunditsira thupi la Ambuye wathu Yesu Khristu m'manda yomwe inakapezeka malo ena mu mzinda wotchedwa TURIN mdziko la Italy.Ndithudi anthu anatsimikiza kuti iyi ndi nsalu yomwe thupi la Ambuye Yesu anafunditsira atamwalira pamene anapachikidwa pa mtanda paja. Nsaluyo inaonetsera madontho a magazi achidziwikire kuti madontho amagaziwo anali a munthu amen analandira zinthu zowawa zimene zinamtengera iye imfa ,munthu ameneyotu ndi Yesu wopachikidwa pa mtanda. Zizindikiro zinaoneka monga chisoti cha minga chomwe anavala ndi misomali m'manja mwake monga zizindikiro za imfa yake.

Anthu ena analankhulapo kuti nsalu zofunditsira thupi la Ambuye Yesu zinaonekazo,zinali za pakati pa zaka monga 16th Century. Ndipo mbali imodzi ya nsaluyo inadulidwa ndikukayesedwa ku LABORATORY (awa ndi malo amene zinthu zosiyanasiyana zimapita kukayesedwa molingana ndi cholinga chake chakafukufuku amene anthu akufuna kumupeza). Ndipo kafukufuku amene anapezeka anali otsimikizira kuti ndi zoonadi izi zinali nsalu zomwe anafunditsira thupi la Ambuye wathu Yesu. Komanso nsalu yomwe inadulidwa ndi kukayesedwayo inaonetsera kuti kachidutswa ka nsalu kamene kanakayesedwa ku malo oyeserayo itagwera pa moto inaperekanso umboni oti inali nsalu yomwe Ambuye Yesu thupi lawo linafunditsidwa.

Posachedwapa kafukufuku wina anachitika pa kachidutswa chomwe chinadulidwacho,ku malo ena oyesera zinthu (LABORATORY), pa nsaluyo panali zizindikiro zina monga udzu ndi zomera zimene zinakakamira pa nsaluyo ndikuti zomera izi zimapezeka mu nthawi yakale ndipo zina mwa zomerazo zinali za mu nthawi ya ma 1st Century,zina mwa zomerazo zinali mtundu wa zomera zimene zimapezeka pakati pa ana a ISRAELI mdziko lawo. Pamenepa mu kafukufuku ameneyu tiona kuti umboni okwanira ukupezeka kuti nsaluzi zinali zomwe anafunditsira thupi la Ambuye Yesu atamwalira pa imfa yopachikidwa pa mtanda. Komanso madontho amagazi amene anapezeka pa nsaluzo atayesdewa anapezedwa kuti anali madontho amagazi osiyana ndi magazi ena onse anthu a pa dziko la pansili.

Kafukufuku akamachitidwa ofuna kuyesa magazi a munthu kuti tidziwe makolo a munthuyo,amaonetsa nthawi zonse bamboo komanso mayi ake ,koma mu kafukufuku amene anachitika pofuna kuona madontho a magazi amene anapezeka pa nsaluyo,anangoonetsera zizindikiro za amayi ake ,koma bamboo wake kafukufuku sanaonetsere kuti bamboo ake anali ndani,izi ndi zomwenso baibulo limafotokoza kuti Ambuye yesu anabadwa mwa mariya mnamwaliyo,koma mwa mphamvu ya mzimu woyera,kutsimikizira kuti Iye anali mwana wa Mulungu wobadwa yekha mwa Mariya mnamwaliyo. Mu bukhu la Yohane chaputala cha 20:1-8, malembo akufotokoza bwino momveka kuti thupi la Ambye Yesu atalitsitsa pa mtanda paja analikulungu ndi nsalu ,nsalu zina anakulunganso nkhope yake,zomwe zikutsimikizira kuti Ambuye Yesu anafunditsidwa nsalu za kumanda pamene anali kuwayika m'manda. Madontho amagaziwa anayesedwa kangapo konse ndipo anatsimikizira kuti anali madontho a magazi a Ambuye Yesu.

Mukafunsa munthu amene sakhulupirira kuti Mulungu alipo,kapena amene samapemphera,kapena amene asali mu Yuda,za nsalu yomwe inapezekayi yomwe anafunditsira thupi la Khristu Yesu,akana kuti nsalu zimenezo si nsalu zomwe anafunditsira thupi la Ambuye Yesu ,koma sangathenso kupereka umboni okwanira angakhale pa chikhulupiriro chawo. Koma funso ndi lakuti, kodi nsaluzi zinakapezeka bwanji mu KAFEDRO wina mu mzinda wa TURIN mdziko la ITALY,kumene ndi kutali kwambiri ndi malire a dziko la ISRAELI ?. Funso ili silovuta kuliyankha monga mukudziwa bwino kuti mtumwi PAULO,anayenda,madera ambiri a maiko a ITALY komanso SPAIN. Pa nsalu zomwe zinapezekazi sipamoneka nkhope ya munthu,kweni kweni,pokha pokha,mutajambula nsaluyo chithunzi cha negative. Mukapanga chonchi mukhonza kumaona chithunzi cha nkhope yomwe ndi ya Yesu mu zaka za ma 1st century.Anthu ambiri amakhulupirira kuti chithunzi cha Yesu pa nsaluyi chinapezeka chifukwa champhamvu yakuwala kwa dzuwa kumene kunaombera pa nsaluyo,ndipo izi zikupereka umboni waukul u kuti Ambuye Yesu anaukadi m'manda muja,monga malemba anena kuti Iye anauka kwa akufa patatha masiku atatu nakhalanso ndi moyo,ndipo anthu oposa 500,anamuona Iye ali ndi moyo atauka kwa akufa.

Baibulo silikufotokoza kuti maonekedwe ache kwa anthu anali kamodzi kapena kangati, koma anthu oposa 500,anamuona Iye asananyamuke kupita kumwamba ,izi sizodabwitsa,ayi kuzimva anthu akulankhula, choncho tsopano mwatha kupeza umboni okwanira pa za nsalu yomwe anafunditsira thupi la Ambuye Yesu yomwe inakapezeka ku KAFEDRO wina mu mzinda wa TURIN mdziko la ITALY. Zili ndi inu kuvomereza izi kapena kutsutsa izi, koma kwa ine ndkhonza kujowa ndi kusangalala kwambiri chifukwa cha nkhani yokondweretsayi, monga malembo anena mu bukhu la YOBU kuti,'' NDIMDZIWA MOMBOLI WANGA KUTI ALI NDI MOYO''.

Ambuye akudalitseni koposa pamene muwerenga chiphunzitso chokoma chotere. Wolemba ndi mkonzi ndi Rev. ROGER ARTHUR KEECH a ku SCOTLAND UK.

tipezeni ife