chichewa   |   english

werengani izi

(read)

UFITI - CHOTCHINGA CHACHIKULU PA CHITSITSIMUTSO CHA MUMPINGO

(Witchcraft - the greatest barrier to revival in the church)

PHUNZIRO 1 - KUKHALA MU UFITI
(Study 1 - Manipulation)

Mukumvetsetsa kweni kweni kwa ziphunzitso izi, panalibe cholinga china chili chonse kufuna kuwulula anthu a mumpingo, azitumiki a Mulungu, kapenanso othangatira kutumikira pa ntchito ya mumpingo, pofuna kuwapangitsa iwo kukhala ngati ochimwa pa maso pa Mulungu. Cholinga chake chenicheni cha ziphunzitsonzi nkufuna kuika pa mbalambanda mzimu wa ufiti ndi kuyamba kuonetsera m'malemba momwe ife tingagonjetsere satana mdani wathu kupyolera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Kodi chotchinga chachikulu choposa zonse mu chitsitsimutso cha mu mpingo ndi chiyani?. Popanda kukayikira kwina kulikonse ndiye kuti ndi ufiti. Pamene munthu wochita masewero okankhana ndi kulimbana alowa m'bwalo navalanso chotchinga kumaso kwake, izi zitanthauza kuti iye akhonza kulimba ndi anthu ochuluka koma iye osazindikirika. Umunso ndi momwe zimakhalira osasiyana ndi mchitidwe wa ufiti- amakhala akusanduka kudzera m'maina ochuluka, mizimu yambiri ya ufiti, imaoneka ngati yosaopsa, koma pamene ufiti uwululika poyera pagulu tikhonza ukhonza kuwonongedwa ndi mphamvu ya mapemphero.

Kutanthauzira kwenikweni kwa ufiti,ndiko kuti, kupangitsa anthu kuchoka mu umunthu ndi cholinga choti adzitumikira iwe molingana ndi cholinga cha ufiti. Pofuna kukhala ndi ulamuliro woposa anthu onse. Kapena kuti udziposa anthu onse mu zochitika zako.

Ngati ufiti sungathe kuzindikiridwa,kapena kuwululidwa mu mpingo,ndiye kuti palibe mpingo umene ungapange zinthu zopambana pokwaniritsa zolinga zake zenizeni za Mulungu. Pali maonekedwe osiyanasiyana a ufiti mu mpingo, nthawi zina anthu ake amakhala owoneka achilungamo kwambiri pamaso pa anthu nachita zinthu zonse mu mpingo za chifundo,koma Mulungu adana nazo ntchito zonsezi.

Pali magulu atatu ochita za ufiti amene akhonza kuikidwa mundandanda wake, awatu ndi : Kukhala mu ufiti, Ulamuliro ndi Matsenga. Tidzaona kupyolera mu maphunziro awa momwe mtundu uli wonse umagwirira ntchito yake. Makamakanso chitsanzo cha ufiti chowoneka bwino m'baibulo ndi pamene tiwerenga bukhu la 1 Samueli chaputala cha 15. Pofuna kumvetsetsa bwino za nkhani ya ufitiyi, pakufunika kuwerenga tsatane tsatane wa nkhani zopezeka ma bukhu awa:

Bukhu la 2 Samueli 15:1-12, tiwerenga nkhani ya Abisalomu,mwana wa Davide yemwe anali chifupi ndi ufumu wa Atate wake,koma iye sanafune kuyembekezera kuti ufumuwo ufike kwa iye mu nthawi ya Mulungu,koma iye anafuna kugwiritsa ntchito anthu ena ndi zinthu zina pofuna kutenga ufumuwo msangamsanga,angakhale anali kudziwa kuti zomwe amachitazo kunali kuyamba mulandu wofuna kulanda boma moukira.Sanafune kuyembekezera nthawi ya Mulungu nafuna kuutenga ufumuwo mwa iye yekha.

Mu nthawi ya kuwukira ufumu wa Atate wake, Abisalomu anadzitengera yekha akavalo ndi mahachi, pamodzi ndi iye ankhondo ake okwana makumi asanu nafulumira patsogolo pake. Amatha kudzuka m'mamawa kwambiri ndi kuima m'mbali mwa msewu wolowera ku chipata cha mu mzinda. Nthawi ina iliyonse anthu akafuna kubweretsa madandaulo pamaso pa mfumu kuti iwathandize pa mavuto awo, Abisalomu amadziitanira anthuwo kwa iye yekha kuti akawathandize pa mlandu wao, nati nawo, "Ndinu ochokera kuti?". Wofunsidwayo namuyankha Abisalomu, "kuti kapolo wanu ali wochokera mu fuko la Israeli". Ndipo Abisalomu anali kumuyankha iye nati," taona, madandaulo ako ndi omveka komanso ndi oyenera,komatu taona palibe munthu aliyense woimirira mfumu kuti akuthandize pa nkhani yakoyi." Ndipo Abisalomu anali kuwonjeza kunena kuti, "Ndikanasankhidwa kukhala woweruza mu dziko lino! Ndipo aliyense amene ali ndi madandaulo,kapena nkhani, bwenzi akumabwera kwa ine, ndipo ine bwenzi ndikuonetsetsa kuti chilungamo chikuchitika pa anthu onse". dzanja lake, namkhudza munthuyo,ndi kumpsopsona. Ndipo Abisalomu anachitenga chinthu ichi mwa nthawi zonse nachichita kwa ana onse a Israeli,womwe ankabwera kwa mfumu kuti athandizidwe pa zovuta zawo. Choncho mitima ya anthu ambiri a Israeli inatsatira Abisalomu.

Koma pakutha pa zaka zinayi, Abisalomu anati kwa mfumu Davide,"Ndiloleni ine ndimuke ku mzinda wa Hebroni kuti kumeneko ndikakwaniritse lumbiro langa ndinali panga pamaso pa Mulungu Ambuye. Pamene ine kapolo wanu ndinali ku Geshuri wa Aramu, ndinapanga lumbiro ili: "Kuti ngati Ambuye Mulungu angandibwenzerenso ku Yerusalemu, ndiye kuti ndidzamulambira Ambuye wanga ku Hebroni". Ndipo mfumu inati kwa iye,"Pita mumtendere". Choncho Abisalomu anamuka ku Hebroni.

Ndipo Abisalomu anatumiza anthu mwachinsinsi, mwa mitundu yonse ya Israeli,ndi kunena kuti, nthawi iriyonse mumva kuwomba kwa lipenga, mudziti, 'Abisalomu ndi mfumu ya ku Hebroni!." Ndipo anthu okwana mazana awiri a ku Yerusalemu anamuka naye pamodzi Abisalomuyo. Iwo anali oyitanidwa ngati,ngati alendo,namuka mwa kachetechete, koma ali osadziwa kuti kumene akupitako kuli zinthu zotani.

Ndipo pamene Abisalomu anali akupereka nsembe,ndipo anatumaza Ahitofeli wa Giloni, phungu wa Davide,kuti abwere kuchokera ku Giloni,mzinda wa kwawo. Choncho chiwembu chomwe amakonza Abisalomu chinali kukulirakulirabe,ndipo omtsatira Abisalomu anali kuchulukirachulukiranso. Abisalomu, ndiyetu amene amayenera kulowa ufumu wa Atate wake, akadzamwalira Davide,koma vuto lake anadzitengera ulamuliro mwa yekha,m'malo moyembekezera pa Ambuye Mulungu, ndipo pamapeto ake anataya mwayi wake wonse,pamene anayamba kugwiritsa ntchito anthu ndi zinthu zina pofuna kupeza mwayi wodzakhala mfumu ya Israeli.

Monga Ambuye Yesu anapezanso,mu nthawi ya utumiki wake pansi pano,ngati mtima wako waikika pamaso pa Mulungu kuti umkondweretse Iye,mosakaika adani adzakuchulukira panjira yako, komatu angakhale utanyozedwa pansi pano pamaso pa anthu, dziwa kuti pamaso pa Mulungu ndiwe wokondedwa kwambiri ndi Mulungu akamakuona Iye pamaso pake. Aliyense amaoneka ngati akulakwitsa. Koma Ambuye akuyang'anatu wina amene alinawo mtima wakudziwitsa za Mulungu ndinso kunkondweretsa Mulungu.

Chimodzi mwa zitsanzo za momwe ufiti umalowera mu mpingo,ndikudzera mwa munthu wina amene alindicholinga chofuna kumwaza mpingo wa Mulungu,kuti potero anthu amu mpingomo asathenso kutsatira m'busa koma m'malo mwake anthu a mumpingomo adzawatsatira iwo,ndipo kenako adzadzitcha okha kuti ndi azibusa mu mpingo watsopanowo,kuti athe kukwaniritsa zolingirira zawo. Mukawonetsetsa zinthu ngati izi, sizikuonetsa kuti umenewu ukhonza kukhala mtima wa munthu wa Mulungu wodzichepetsa, ndipo anthu oterewa chimene amafuna pa moyo wao ndi kufuna kudzikweza okha, osati kukwezedwa ndi Mulungu.

Zitha kukhala zotheka, kuti m'busa ameneyu, pozikhazikitsa yekha kukhala m'busa mu mpingo wotere, vuto lomwe lingabwere ndilo kuti adzangokhalira kutemberera anthu omwe sanamvere zofuna zake monga m'busa.angakhale kuti sakunena zinthu zonsezi zotemberera akhristu, koma nkutheka kuti mwina kayendetsedwe kake ka mpingowo, katha kukhala kosadziwika bwino,chifukwa pena zidzikhala ngati akulondola kapena akulakwitsa. Tsono kuteroko ndiye kuti sikumvera Mulungu pa utumiki ayi, koma uku ndiko kupangitsa anthu kuti akhale chimene iye ali,ndipo mwakutero umenewu umakhala ufiti ndithu. Anthu ena adzangoti,ubusa uwu ndi wina wake,osati umene akuchita anthu ena. Choncho uku ndiko kupangitsa zinthu kukhala molakwika, ndipo ndi chifukwa chake Mulungu akuwutcha kuti ndi Ufiti.

Chitsanzo china cha momwe zinthu zina zimagwirira ntchito, ndi momwe utumiki woyendayenda,kapena abusa osakhazikika amachitira ndi nkhosa zawo, pena kuzikalipira zikapanda kuwapatsa ndalama zochuluka,ponena zinthu za mabodza tsono kumati, "Tikuyenera kupeza ndalama pa mpingo pano, za chitukuko cha pa mpingo, zokwana $10,000 dollars. Ndiye tsono atumiki abodzawa amayamba ndi kumanenera mauneneri abodza, nkumati,"Eyi, m'bale Thomas, Ambuye akundilankhula pano za inu kuti muyenera kuyambapo kupereka chopereka chachitukuko chokwana $1,000 dollars, zamveka kodi?"

Anthu ochuluka sakonda kuwayalutsa abusa pa gulu, abusawo,akanenera zinthu za bodzazo,iwo amangolembatu cheke,pofuna kupewa zinthu zina za manyazi zomwe zingamachitike mumpingomo. Ukutu ndiye timakutcha kuwachenjerera anthu, ndi bodza ngati njira imodzi yofuna kupeza ndalama, choncho zoterezi zimakhala pansi pa zochitka za ufiti,amene ali machenjerero a woipayo. Chodziwika bwino ndi chakuti Mulungutu safuna kuti inu mudzimuthandizira kupeza thandizo la ndalama zomangira tchalichi. Iye ali wakutha mopambana muja kupanga njira zopezera ndalama zoposa mathandizo amene anthu amathandiza pa mpingo.

Chitsanzo china cha chikhalidwe cha ufiti, tichipeza pa bukhu la 1 Mafumu chaputala cha 21:1-16. "M'mbuyomo tiwona nkhani ina yomwe ikulankhula za munda wa mpesa wa Naboti wa ku Yezreeli.Munda wa mpesa unali mu Yezreeli,pafupi ndi nyumba ya chifumu ya Ahabu mfumu ya ku Samariya. Ndipo Ahabu anati kwa Naboti,"Ndipatse munda wako wa mpesa ndidzalemo ndiwo za masamba,pakuti uli pafupi ndi nyumba yanga. Mosinthana, ndi dzakupatsa munda wa mpesa wina, kapena ndidzalipira malipiro a mtengo wake wa mundawo, momwe unganenere ndalama zake.

Koma Naboti anayankha mfumu nati,"Ambuye Mulungu sakundilola kuti ndipereke kwa inu mfumu cholowa cha makolo anga." Ndipo Ahabu ananyamuka napita kunyumba ali wopsa mtima ndi wokwiya kwambiri,chifukwa Naboti mu Yezreeli anati,"sindingapereke kwa inu cholowa cha makolo anga". Mfumu Ahabu anagona pa kama wake nayang'ana kumbali nakana kudya mkate. Ndipo mkazi wake Yezibeli analowa namfunsa iye, nati kwa iye, muchitiranji msunamo,kuti mukana kudya mkate, Mulekerenji kudya inu mfumu?

Koma Naboti anayankha nati kwa iye,"Chifukwa ine ndinati kwa Naboti mu Yezreeli, ndigulitse munda wako wa mpesa,kapena ngati ungafune ndikupatse munda wina wa mpesa." Koma iye anati sindingakupatse iwe munda wa mpesa. Ndipo Yezeberi mkazi wake anati, "Kodi umu ndi momwe inu muchitira mu Israyeli muno,monga mfumu?. Tadzukani nimudye!. Sangalalani. Ndikupatsani inu munda wa mpesa wa Naboti mu Yezreeli.

Choncho mkaziyo analemba makalata mudzina la Ahabu,naikamo chosindikiza pa makalatapo,natumiza kwa akulu akulu ndi amaudindo, wokhala naye pa modzi mu mzinda wa Naboti. M'makalatawo iye analemba kuti, mulengeze tsiku la kusala kudya ndipo mulole Naboti,kukhala pooneka ndi anthu. Koma muike anthu oipa kwambiri odziwa kupeka mabodza pafupi ndi mpando wa Naboti, ndipo amunamizire kiti Naboti, watemberera dzina la Mulungu wake wa Israeli,pamodzi ndi mfumu Ahabu. Ndipo mudzimtulutsa kunja kwa mudzi ndikumponya miyala mpaka atafa.

Motero akulu akulu okhala mu mzinda wa Naboti anachita monga Yezeberi ananena nawo m'makalata womwe iye analemba.Ndipo iwo analengeza kusala kudya, namukhazuka Naboti pamalo oonekera pamaso pa anthu. Ndipo anthu awiri oipawo,anadza nakhala moyang'anana ndi Naboti,namnamizira mulandu pamaso pa anthu,nati, naboti watemberera Mulungu,pamodzi ndi mfumu".

Choncho anamtenga namtulutsira kunja kwa mudzi,namponya miyala nafa.Ndipo iwo anatuma mawu kwa Yezeberi,Naboti waponyedwa miyala ndipo wafa.Ndipo pamene Yezeberi anamva kuti Naboti waponyedwa miyala nafa,anamuza Ahabu,"Dzukani mfumu nimutenge munda wa mpesa wa Naboti mu Yezereeli umene anakukanitsani kugula uja. Pakuti iye salinso ndi moyo,koma wafa. Ndipo pamene Ahabu anamva kuti Naboti wafa, iye andzuka nathamangira kukatenga munda wa mpesa wa Naboti.

Tikudziwa kuti umu ndi momwe anthu ena amachitira, ngati sangathe kupeza chinthu mwa njira yovomerezeka,amatha kugwiritsa ntchito njira zosavomerezeka, angakhale kuti ndi kupha kumene akuchitako. Mtumwi Yakobo anali ndi liwu limodzi kapena awiri,za anthu amtundu wotere, mu bukhu la Yakobo chaputala cha 4:1-10

"Kodi nkhondo ndi mikangano zichokera kuti pakati panu? Kodi izo sizichokera ku zikhumbokhumbo zochitika mkati mwa inu?. Mumakhumba kukhala ndi zinthu koma simukhala nazo,ndiye m'malo mwake mumapha.Muchita msanje, koma simungakhale nazo zimene muzifunazo. Simukhala nazo chifukwa choti simupempha Mulungu. Pamene mupempha,simulandira,chifukwa mupempha ndi malingaliro olakwika kuti mukachimwaze ku zikhumbitso zanu. Achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wopanga ndi dziko umathandauza udani ndi Mulungu?. Choncho aliyense amene asankha kukhala bwenzi ndi dziko lapansili apanga udani ndi Mulungu, kodi kapena muyesa malembo angolankhula chabe kuti Mzimu achita msanje mwa inu chifukwa Iye akhala mwa inu?. Koma Iye atipatsa ife chisomo chochuluka. Ndi chifukwa chake malemba anena kuti,"Mulungu atsutsana nawo odzikuza,nawonetsera kuchuluka kwa zisomo kwa iwo odzichepetsa.

Dziperekeni nokha kwa Mulungu, mkanizeni satana,ndipo iye adzakuthawani inu. Yandikirani kwa Mulungu ndipo Iye adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja inu ochimwa, dziyeretseni mitima inu anthu amitima iwiri inu.Pangani chisoni,namulire. sinthani kuseka kwanu ndi kulira,ndi chimwemwe chanu chisanduke chisoni. Dzichepetseni nokha pamaso pa Mulungu,ndipo Iye adzakukwezani mu nthawi yake.

Anthu enatu pamene akhala zolingalira zawo ndi zakupha,m'masiku ano otsiriza, izi ndi zachidziwikire tikamamva nkhani zosiyanasiyana zimene tikumamva kawirikawiri, uwutu ndiye timati, ufiti,kufuna kutenga madalitso mosalungama pa zinthu zomwe umayenera kukhala nazo munjira yoyenera, motero umapanga izi mwa chifuniro chanu, angakhale chinthu chomwe umayenera kukhala nacho,ngati Mulungu wakuletsa kukhala nacho panthawiyo,Iye Mulungu namakonza nthawi yovomerezeka, umayenera kumumvera Atate. 1 Akorinto 7:1-5,tiwerenga kuti, "tsopano pa zifukwa zomwe mwalemba, ndiye ndi kwabwino mwamuna kukhala osakwatira. Koma chifukwa cha zilakolako,za mthupi ndiye kuti mwamuna akhale ndi mkazi m'modzi wamwini yekha,nayenso mkazi akhale naye mwamuna m'modzi wa iye yekha.mwamuna ayenera kukwaniritsa zinthu zonse zofunikira pa mkazi wake,chimodzimodzinso,mkazi akwaniritse zofunikira zonse kwa mwamuna wake.

Mkazi alibe ulamuliro wathupi lake payekha,koma alipereka ilo kwa mwamuna wake,momwemonso naye mkazi alibe ulamuliro ndi thupi lake payekha, koma alipereke ilo kwa mkazi wake lonse lamtunthu. Musakanizane wina ndi mnzake, pokhapokha pakhale kugwirizana nonse,komanso mwa kanthawi. Kuti potero mukazipereke nokha ku moyo wa pemphero. Ndipo bwerani pamodzi kuti satana asathe kukuyesani,posowa kudziretsa nokha.

Zadziwikanso kuti akazi ena ali ndi moyo wangati ufiti,kotero amakaniza azimuna awo, ufulu achite, ndiye kuti akapanda kuchita zimenezo ndiye banja palibenso usiku, Awansotu ndi machenjerero. Momwemonso nkhani ya Ahabu ndi Yezeberi,mbali zonnse zikuyenera kulapa pamaso pa Mulungu. Yezeberi pokhala ali ndi kupha mu mtima mwake,polakalaka kupha chifukwa cha munda wa Naboti womwe sakadatha,kusinthana.

Munthu wina anali kulankhula posakhalisapa, kuti banja ndi umodzi osasiyanitsidwa, kodi awanso si mawu amene malemba anena ku Aefeso 5:21-33,ndipo tiwerenga motere:Dziperekeni wina ndi mnzake, monga mwa kulemekezeka kwake kwa Yesu Khristu. Akazi inu mverani amuna anu,amuna inu kondani akazi anu,monga mukhaliranso kwa Khristu Yesu. Pakuti mwamuna ndi mutu wa banja, monganso khristu ali mutu wa mpingo,thupi lake, amene Iye ali mpulumutsi wa anthu onse. Tsopano monga mpingo udzipereka kwa Yesu Khristu,momwemonso akazi inu mverani amuna ainu nokha. Amuna inunso kondani akazi wanu monga Khristu anakonda mpingo wake,nadzipereka yekha kwa iwo kukakonzera mpingo ku chilunga chonse,ndi kuwusambitsa ndi mwazi wa chiyeretso kudzera m'mawu ake a Mulungu,kukauonetsera kukhala wowala koposa,opanda banga pena pali ponse,koma oyera ndi opanda chilema.

Moteronso,amunanso akonde akazi awo monga thupi limodzi. Pakuti iye amene akonda mkazi wake akondanso thupi lake. Komanso kuwonjezera apo,palibe munthu yemwe akhinza kudana ndi thupi lake lomwe, koma iwo alisamala ndi kulidyetsa thupi lawo, monganso Khristu Yesu amaukonda mpingo,pakuti ife tili ziwalo za thupi lake.

Tsopano sikufunikanso kuti inu amuna muzimenya akazi anu,mu dzina la chipembedzo china chili chonse,koma tichite monga Khristu Yesu anakhanzikitsiratu zinthu zonse pa chiyambi,kuti ngati banja ndiye kuti mwamuna azikhala pansi ndi mkazi wake ngati pali zinthu zolakwika nakonze zimenezo. Ndipo pamene chiganizo chachitika (mwachiyembekezo monga zotsatira zake za kukambirana awiriwo,) tsono ukhale udindo wa mwamuna, kuonetsetsa kuti ngati pali zinthu zina zalakwika,akhonze zimenezo.

Sikuyenera kuti mwamuna asamvetsere zina mwa mfundo zimene mkazi wake akupereka m'banja, ayi komatu atsatire bwino, lomwe kuti pakutha pa zonse mwamuna akhale ndi udindo wopanga chiganizo chotsiriza monga mutu wa banja. Mwatsoka lakenso, pali amuna ena kamba kosatha kuchita chiganizo ngati munthu wa mwamuna,zinthu zambiri zimayendetsedwa ndi mkazi chifukwa cha kufooka kwa mwamunayo, izitu sizofunikira monga banja, mwamuna ndiye mutu wa banja choncho wayenera kukhala pa tsogolo pa mkazi wake. Chitsanzo cha zimenezi ndi zina mwa zimene zikuchitika m'manyumba ambiri nthawi ndi nthawi, kupezeka kuti amayi pa nyumba amalephera kuchita chiganizo nthawi ina pa okha, pazinthu zazing'ono, koma mpaka amadikira a bambo kubwera nkumati bambo ndi amene angakonze zinthu.

Ngati chinthu china chilakwika (malingana ndi a bambo a panyumbapo), pakuti mwina vutolo lachitikira amayi,chifukwa choti chiganizo chawo ndi chimene chachititsa kuti,pachitike vuto, ndiye a bambo nawonso amangozisiya kuti kaya azionera okha,pamene kutengera ndi m'mene baibulo likulankhulira za banja, ngati zinthu ziwonongeka kamba koti a bambo analekerera vutolo,kuwasiyira amayi okha, Mulungu ndiye kuti amadzudzula a bambo chifukwa bambo panyumba ndiye mutu wa banja. Zikomo kwambiri, phunziro lathu lachiwiri pa mutu womwe tikulemba wa Ufiti ndi chotchinga chachikulu mu mpingo pa chitsitsimutso.

tipezeni ife