chichewa   |   english

werengani izi

(read)

UFITI - CHOTCHINGA CHACHIKULU PA CHITSITSIMUTSO CHA MUMPINGO

(Witchcraft - the greatest barrier to revival in the church)

PHUNZIRO 2 - ULAMULIRO
(Study 2 - Domination)

Mateyu chaputala cha 20:24-28, tikuwerenga kuti Ambuye anayitana ophunzira awo pamodzi atatha kupempha mayi am'modzi wa ophunzira ake. Zotsatira zake za kupemphaku zinapangitsa kuti ophinzira ena akhale okwiya, choncho Iye anati kwa iwo, "Pamene ophunzira khumiwo(10), anamva izi anali okhumudwa ndi ophunzira awiriwo amene mayi wao anapempha Ambuye Yesu, zokakhala nawo ku paradiso ndi Yesu, ndikuti wina akakhale kudzanja la manja ndi wina kudzanja lakumanzere mu ufumu wakumwamba.

Ndiye Ambuye Yesu anawaitana ophunzirawo nati kwa iwo, "mukudziwa kuti akuluakulu a mitundu amasenzetsa anthu awo katundu wa chilamulo chawo, ndi amaudindo awo akuluakulu amachita ulamulironso pa iwo. Koma inutu sizili choncho, koma tsono iye amene afuna kukhala wa mkulu mwa inuyo yemweyo akhale wotumikira pakati panu, ndiye amene afuna kukhala woyamba pakati panu yemweyo akhale ngati kapolo wotumikira anthu ena- monga mwana wa munthu sanadza pansi pano kudzatumikiridwa ndi anthu koma kuti iye akatumikire anthu ku dziko la pansi, ndikupereka moyo wake kukhala nsembe yowombola anthu ochuluka ku dziko lapansi.

Ndondomeko za katumikiridwe kamene Ambuye Yesu amalongosolera ophunzira ake, ndi kamene Iye mwini akuyembekezera kuti ife monga ophunzira ake tikachite chimodzimodzi, ndi kudikira kufikira nthawi yoikika itakwana. Tikayang'ana moyo wakudziko lino lapansili tiwona kuti mfulu za dziko lino lapansi likalemba ntchito anthu owagwirira ntchito, amawafulumizitsa pogwira ntchito zawo mwa nkhanza, pofuna kuwapangitsa kuti akhale pansi pawo ndi kumvera iwo kwa mtunthu, ndi kulandanso ufulu wa antchito awo. Izitu zili chomwechi ndi anthu ochuluka amene akugwira ntchito, akumachitiridwa zinthu zambiri. M'mbuyomu kunali kosaloledwa kuti munthu adzigwira ntchito pa nthawi yopumula, koma masiku ano muona kuti anthu ambiri akumatha kubwera ndi chakudya kuchoka nacho kunyumba, ndipo ikafika nthawi yopumulira amapezeka kuti akulandira chakudya uku akupitiriza kugwira ntchito. Kuwonjeza apa angakhale anthu amapezekabe, akugwira ntchito pa nthawi yopumulira chomwechi, samalandinso ndalama yopitirizira kugwira ntchito pa nthawi yosamvomerezekayi.

Koma Ambuye Yesu anafunitsitsa kuwaphunzitsa ophunzira awo, kukhala moyo wa chilungamo ndi wosakondera, kuti ophunzirawo akhale osiyana ndi antthu a kudzikom lino lapansi. pa nthawi imeneyo, womwenso anali pansi pa mphamvu ya ulamuliro wa Chiloma. Mukhonzanso kuona kuti pali maiko ena masiku ano amene akupitiriza kuchitira anthu ambiri nkhanza, kotero kuti sipakhalanso kokasuma nkhani za nkhanza zotere. Mwatsoka lake angakhale mipingo ina masiku ano sitsata chilungamo pofuna kuthandiza anthu osowa ndi osautsidwa, koma mutadzifunsa mwa padera, chiganizo chomwe cha pangidwa ndi m'busa kapena mtsogoleri wa mpingo, muona kuti akalengezetsa zinthu zina mu nthawi ya mapemphero, zimene alengeza zija anthu ena sakudzidziwa ndi pang'ono pomwe, anthu ambiri, amakhala akudabwa kuona kuti zolengeza zangochitika anthu ena osadzidziwa, ndipo chifukwa chakuwaopa azibusa oterewa, anthu ambiri amangovomereza chili chonse osatsutsana nawo.

Umenewu si ufulu umene Ambuye Yesu anatifera nawo pa mtanda paja, zoterezi zikungowonetsa kuti zikutsutsana ndi momwe Ambuye Yesu amafunira kuti ife monga ophunzira ake. Mu mpingo weniweni wa chikhristu, ngati pali ena amene sakugwirizana ndi mfundo zina, zomwe azitsogoleri akuoanga, apa zimafunikira kuti Abusa kapenanso atsogoleri ena akhale omasuka popereka mpata kwa anthu aja kuti amvenso maganizo awo, ndi otani pakayendetsedwe ka mpingo. Ndipo nthawi zina tikawalola anthu ngati amenewa kupereka maganizo awo, mudzaona kuti zinthu zambiri pa mpingo zikuyenda bwino.

Azibusa ayenera kuthandizabwino, anthu onse mu mpingo ndi chikondi komanso kudzichepetsa, limenenso linali khalidwe lake la Ambuye wathu Yesu, angakhale pa nthawi yomwe mayi wa ophunzira ake anamufunsa pempho losayenera, koma Iye sanawayankhe mayi wake wa ophunzirawo zokhumudwitsa, anawayankha moyenera. Njira yokhayo yopezera chipambano pa mpingo ndi ndi kuwalimbikitsa a khristu onse ndi kuwasonyeza kuchita zinthu za bwino, koposa kuti anthu aja tingowayankha zosamangirira miyoyo yawo.

Bukhu la Agalatiya chaputala cha 5: 1, tiwerenga kuti, pakuti Khristu Yesu anatipangira ufulu pofuna kutipulumutsa ife tonse. Imani nji pamaso pake osagwedezeka, ndipo musadzimvekanso nokha goli la ukapolo". Momvetsa chisoni chifukwa akhristu akhala chete ndinso kufooka moyo wa lerowu, kotero zapangitsa kuti tsopano m'malo mwa ana a Mulungu kukhala ochitachita, dziko lapansi ndilimene likuwoneka kuti lilipatsogolo kuchitachita zinthu zosiyanasiyana, izitu makamaka zikuchitika kwambiri m'maiko amene anthu sapatsidwa ufulu wolankhula za kukhosi kwao.

Pafupifupi mwezi uliwonse anthu ambiri m'maiko a kumadzulo amanka nataya pang'onopang'ono ufulu wawo umene umachotsedwa kwa iwo ndi maulamuliro a boma awo amene amanena kuti ndi ma boma otsatira ulamuliro wa demokalasi. Chifukwa choti pali anthu ochepa amene akufuna kuti akhonza kuima ndi kutsutsana ndi mchitidwe woponderezana, ndikuyamba kuwadziwitsa anthu za kufunikira kwa ufulu wao, ndinso kuwadziwitsa kuti adziwe chikuchitika ndi chiyani ku dziko, koma ichi sichili pa anthu okha ayi komanso angakhale maiko ambiri a kumadzulo nawonso akudandaula chifukwa cha kuponderezedwa, ndipo izi zili kuchitika opanda owamenyera nkhondo.

M'maiko ena omwe ankadziwika kuti ndi a chikhristu kalero, muonanso kuti angakhale aphungu akunyumba ya malamulo, akamafuna kupanga malamulo amapanga mosemphana ndi chifuniro cha Mulungu chimene chili m'baibulo, chonsecho muona kuti ana a Mululungu omwe atchedwa ndi dzina loti ndi akhristu samaima ndi kutengapo gawo lofuna kumenyera nkhondo ufulu wao ngati akhristu. Tikaonetsetsa zoterezi sikuti ndi maiko a kumadzulo okha ayi, komanso angakhale maiko ambiri pa dziko lino lapansi izi zikuchitika.

Pakadali pano palinso mzimu wa mantha ngakhale malo antchito, muona kuti mabungwe omenyera anthu pa ntchito amene, ndi amenenso akuononga zinthu zambiri, izi zili chomwechi ngakhale maiko a ambiri akumadzulo anthu ambiri amaumirizidwa kugwira ntchito nthawi yaitali ndi cholinga choti pakutha pa nthawi yawo yogwirira ntchito kutsogoloko, adzalandire ndalama zochuluka, komanso amaopsezedwa ndi owalamulira awo kuti akapanda kuero ndiye kuti ntchito yawo ikhonza kutha.

Nditakufunsani inu, kodi zinthu za mtundu wotere, zinayamba kukuchitikirani inu, zoona zikhonza kukuchitikirani inu, mwanjira ina ili yonse, izinso zikhala ngati kalilole wotithandiza kuyang'ananso pa mbuyopo, pamene Mose anali kupita ku Aigupito kukatulutsa ana a Israeli amene anali muukapolo, ndikuti akakhale nthawi yakuyenda mu chipululu muja ana a mulungu. Eksodo chaputala cha 5: 1-9, nkhaniyi itiphunzitsanso podziwa momwe anthu a ku Aigupito ankawafulumizitsa ana a Israeli powagwiritsa ntchito, kuti anafika powaonjezera ntchito zogwira kuposa poyambapo, chifukwa Mose anadziulula kuti anatumidwa ndi Mulungu kuti adzapulumutse ana a Israeli, m'manja mwa Falao mfumu ya Aigupito.

Ndipo kenako Mose ndi Aroni anapita kwa Falao, nati naye, "awa ndi mawu amene Mulungu wa ana Israeli watituma kwa inu, kudzalankhula nanu kuti, "ulole ana anga kupita kuti akanditumikire ine muchipululu, ndipo Falao anati kwa Mose "Mulungu ndi ndani?". kuti ndikamumvere Iye, ndikulola ana Israeli kutuluka mdziko la Aigupito?. Sindimdziwa Mulungu wa Israeli, ndipo sindingalole kuti Israeli apite muchipululu. Koma Mose ndi Aroni anati kwa Falao, Mulungu wa Aheberi anationekera ife nalankhula zonsezi.

Tsopano tiloleni ife masiku atatu kumuka mchipululu kukapereka nsembe kwa Mulungu wathu, pakuopa kuti Iye angatikanthe ndi miliri yoopsa kapenanso kuti angatikanthe ndi lupanga, "koma mfumu ya ku Aigupito inati kwa Mose ndi Aroni, chifukwa chiyani mukuwachotsa anthuwa ku zintchito zawo?. Bwererani ku zintchit zanu!". Ndipo Falao anati, "taonani, anthu amdziko tsopano achulukana kwambiri, ndiye inu mukuwaletsa ana a Heberiwa kugwiri ntchito".

Ndipo kuyambira tsiku lomweli Falao analamulira akapitao, ndi onse oyang'anira a Israeli pogwira ntchito, "Musamawapatsanso ana a Israeli udzu wogwirira ntchito poumbira njerwa kuyambira lero, dziwasiyani kuti adzikamweta udzu woumbira njerwa wokha, koma muwonetsetse kuti muyeso wa njerwa zoumbidwa patsiku ukhale womweo, musawachepetsere muyeso wao wa ntchito youmba njerwa, ndaona kuti ali ndi ulesi, ndichifukwa akulira kuti adzipita mchipululu kuti akaperekere nsembe kwa Mulungu wao, kulitsani muyeso wa ntchito zawo kuti amve kuwawa, ndi kuti potero akhale akugwira ntchito tsiku lonse osapuma, ndipo musawamvera chisoni pamene akunamizani.

Uwu ndi mtundu wa machitidwe umene anthu ogwiritsa ntchito mphamvu za ufiti, amachita pa ana a Heberi, pakuti chikhalidwe champhamvu yaufiti, chimagwira ntchito kupondereza ndi kuphwanya ufulu wa osautsidwa, kuti mizimu yawo ikakhale yosweka ndi kukhala anthu amantha kotero kuti sangathenso kudzuka ndi kudandaula pa vuto lawo. Lerotu anthu ochuluka akunka nazunzidwa ndi ziphinjo zosiyanasiyana m'malo a pantchito koma osayerekeza kufotokoza za mabvuto awo kwa anthu chifukwa chakuopa kuti angachotsedwe ntchito.

Tiwonanso mu bukhu la Eksodo, kuti ufiti munjira yaulamuliro ndi kuponderezana umachitika mu nthawi ya Mose. Tiwonanso kuti ufiti unali kuchitika ndi anthu amene Danieli anali kukhala nawo ku dziko la Babulo, kumene ana a Israeli anakalangidwa ndi Mulungu kamba kakusamvera kwa zaka makumi asanu kudza awiri(70). Koma nkhani ya fano lija losema limene mfumu ya ku Babulo analamulira kuti anthu adzilambira, ikhalanso yosangalatsa, kuti chosema fano losema limene munthu wa uchimo analipanga lilembedwa mu mbiri yake m'bukhu la Chibvumbulutso chaputala cha 13, ndipo ili nkhani yofanana.

Choyamba tiyeni tiwone Danieli, pa nkhani ya fano losema la golide lomangidwa ndi mfumu Nebukadinezara mu Babulo, liene linamangidwa ndi mfumu Nebukadinezara ku Baul, Danieli chaputala cha 3: 1-7, "Mfumu Nebukadinezara anali ndi fano losema, milingo yokwana 90 kutalika kopita m'mwamba, ndinso milingo yokwana 90 kupita 'm'mbali mwake, naliimika mu chigwa cha Dura mu Babulo. Ndipo mfumu Nebukadinezara analamulira nduna zake zonse pamodzi, Ngwazi, Nduna za zikuluzikulu, Akalonga ndi Ndoda zikuluzikulu, Akazembe ndi Asungi chuma, Oweruza, ndi onse omva ndi kuweruza milandu yosiyanasiyana, ndi akuluakulu amzigawo zones za mdziko lake. Iwo anamuka kokakhala nawo pamwambo wa kukhanzikitsa fano lamkuwalo limene mfumu Nebukadinezara analikhanzikitsa ku chigwa cha Dura.

Ndipo pamene nthumwi zones za mfumu zinafika kumalo amwambo wokhanzikitsa fanolo, ndikuima patsogolo pa fanolo, ndipo kunali munthu wakuomba lipenga pamaso pa anthu onse ndi mfumu Nebukadinezara, kukonzekeretsa anthu onse ndi kuomba lipengalo ndi mawu okweza, pamenepo anthu amafuko onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi zilankhulo zawo, nalamulira kuti, pamene mudzamva kuombedwa kwa lipengalo, motsatana ndi zitoliro, ndi azeze, ndi malingaka, pamodzi ndi zipangizo zamitundu yonse zidzayimbidwa. Mwachangu pamene nyimbo ziyamba kuyimbidwa, anthu nonse mukudziwitsidwa kuyamba kulambira, ndi kulipembedza fano la golidilo, limene mfumu Nebukadinezara analiimika kuti anthu mulilambire.

Koma pakapezeka munthu wina wosalambira ndi kupembedza fanolo, adziwe kuti adzaponyedwa mung'anjo yoyaka ndi moto. Choncho pamene anthu onse anamva kulira kwa zitoliro ndi azeze zoyimbidwa pokonzekera kulambirako, anthu onse amitundu yonse, ndi zilankhulo zonse, anagwada pansi naymba kulamira fanolo, Kuyankhula zinthu zoona, uwu ndi mchitidwe waufiti, wa mgulu lotchedwa Ulamuliro wopondereza anthu(Domination), umene uli ndi chikhalidwe cha ufiti.

Tsono tiyeni tionenso bukhu la Chibvumbulutso(Revelation), chaputala cha 13, kumenenso kwalembedwa za fano lina lomwe likuumbidwa, lotchedwa "Chonyasa Chobalalitsa anthu ndi kuwapondereza", monga Ambuye Yesu analankhulanso za icho. Padakali pano kuumbidwa kwa fano ndi kulilambira kwake, kuthandauza kukhala mu ukapolo kwa anthu, posowa ndalama, ndinso kuwakakamiza anthu kulandira malipiro ochepa a pamwezi, kuti tsono mathero azonsezi anthu ochuluka akalandire lemba pa mphumi pawo la chilombo chotuluka m'mdzicho ngati anthu akufuna kugula ndi kugulitsa malonda osiyanasiyana.

Ndipo iyenso anakakamiza anthu okhala pa dziko lonse lapansi, wamng'ono ndinso wamkulu yemwe, wosauka, ndi olemera achuma, mfulu ndi akapolo, kulandira chilembo cha cha fanolo, kudzanja lamanja, kapena pamphumi, kotero kuti wina asathe kugula kapena kugulitsa malonda pokhapokha atadinditsa chilembocho pa mphumi pake kapena, pa dzanja la manja, chimene chilli mudzina la chilombo, kapena nambala ya dzina lake. Apa tsono nzeru ikufuula kuchenjeza anthu onse, ngati pali wina wakudziwitsa zinthu izi, ayambe kuwerenga nambala ya chilombo, pakuti iyi ndi nambala ya munthu, ndipo nambala yake anthu musasokonezeke ayi, ndi666".

Apa tikuona kuti, si mfumu ya ku Babulo imene ikuyambitsa chilembo cha 666, koma munthu wa kudziko lapansi akufuna atenge mphamvu ndi ulamuliro kudziko lonse kudzera mudzilakolako zonyasa. Mwa ichinso tiona kuti Ufiti mu gawo la Ulamuliro woipa(Domination) unayamba kuchitika ndi Aigupito, Ulamuliro wa Chiroma, anthunso alero, angakhale kuti zili kuchitika apa ndi apo, koma tionanso kuti kutsogoloko, zinthu zidzakula msinkhu, ngakhale kuli chimaliziro cha dziko lino lapansi, nthawi ikudza pamene woipayo adzaonongedwa kotheratu ndipo sadzakumbukirikanso, ndi anthu mpaka kale.

Tionanso m'mene mchitidwe wa ufiti ukupitira patsogolo, ndi momwe ukugwiritsiridwa ntchito, mdziko lapansili, lero muona kutiso kwakukulu ukuchitika ndi anthu otchedwa kuti ndi akhristu, umu ndi momwe zinlili nthawi ya mchipangano cha kale mu bukhu la Eksodo m'masiku a Mose, kufikira mu bukhu la Chibvumbulutso(Revelation), limene liri bukhu lomwe likulongosola za momwe zinthu zidzakhalire mtsogolomo, mu nthawi yotsiriza. Makamakanso ufiti tikuwuona m'magawo ake onse kuchuluka ndi kuchulukira kwake m'Madera onse amene tikhalamowa, izitu zithandauza kuti tili m'masiku otsiriza.

Kodi nanga ufiti, ukutha bwanji kukhala chinthu chotiponderaza mu ulamuliro wa kumidima?, Mwamwayi tikhonza kuona kuchokera mu chipangano chakale bukhu la Genesesi, chaputala cha 3: 3, chioneka kuti chitithandiza kutitsogolera pa maganizo abwino. Vesi imeneyi tiwerenga kuti, Taonani, ndipo njoka inali yochenjera koposa nyama zinse za mtchire, zimene Mulungu anazilenga. Ndipo njokayo inati kwa mkaziyo, kodi Mulungu anati, "Musadye chipatso china chili chonse cha m'mundamu?".

Kodi inu tamvani, baibulo likamanena za njoka, limakhala likulongosola momasulira kuti njokayo ndi satana, mukhonza kuona m'mene Hava anayesedwa ndi njoka, zinampatsa kukhala moyo wokaikira Mulungu ndi mawu ake omwe.

Angakhalenso lero lino machenjerero amtundu womweu, akugwira ntchito pa anthu ambirimbiri osawerengeka, ngati mdani satana angathe kutipatsa malingaliro achikayikiro, pa mawu a Mulungu ndiye kuti tsono tikhala anthu opanda chitetezo china chili chonse pa zinthu zonse zimene satana angatichitire. Tikhonzanso kuona umo Mulungu analankhulira mu nthawi ya Adamu, za matemberero, umboni ulipo kuti mawu a Mulungu akuchitika ndi kukwaniritsidwa.

Kuyambira nthawi imeneyo tiona kuti thupi ndi malingaliro a Adamu ndi hava zinayamba kuonongeka, angakhale mwa chisomo cha mulungu, zinatengabe nyengo yaikulu, yomwe iwo anadutsa mu zambiri naphunzira zinthu zochuluka, komabe mawu a Mulungu anakwaniritsidwa kuti munthu adzafa ndithu. Choncho tionanso kuti kukhala moyo wokayikira mawu a Mulungu, ndiye kuti machenjerero a satana amatitsegukira nabalapo chipatso cha imfa.

Anthu ambiri lero(mwatsokanso nakhala iwo anapita ku maphunziro a ubusa), ndi amene alinso patsogolo kukhala moyo wachikayikiro, namanena kuti Yesu sanabadwe mwa mariya namwaliyo, namakayikiranso, angakhale kubadwa kwache, ena akayikiranso kubadwa, nakayikiranso imfa ya Ambuye Yesu ya pa mtanda, ndiponso amakayikira kuuka kwache m'manda muja. Ngati sitikhulupirira choonadi cha mawu awa, monga mawu anenetsa poyera kuti Yesu ali mwana wa Mulungu, ndiye kuti chikhulupiriro chathu chili chopanda pake, ndipo Yesu Khristu sangathe kupanga kanthu kalikonse pa ife, pamenenso chikhulupiriro chathu chili cha kufa pakutinso posakhulupirira ife mphamvu yake timuyesa Iye kuti ali wa bodza.

Vesi ya 16 mu chaputala cha Genesesi 3, tiwerenga za chilango choyamba, chimene anapereka kwa Hava, potenga mbali kusamvera Mulungu, ndi mawu ake. Ndipo kwa mkaziyo anati, ndidzapereka kuwawa kwakukulu pa nthawi yako yakubereka, ndi kumva zowawa za kubereka, ndi kukhumba kwako kudzakhala mwamuna wako koma iye adzakhala nawo ulamuliro pa iwe.

Ndi mawu okhulupirika kwambiri, thandauzo la mawu awa kuti "kukhumba kwako kudzakhala mwamuna wako", awa ndi mawu amene atanthauza kuchokera mu bukhu la Chiheberi, "udzakhumba kukhala womulamulira iye, ndi kulanda mphamvu zake ndi ulamuliro wa mwamuna wako, koma sidzidzatheka.

Pali azibambo ena monga talankhula kale m'mbuyo muja, kuti ali afooka mudzochitika zawo koposa akazi awo, nalola akazi awo kuti adziwalamulira. Zimatheka nthawi zina kuona a bamboo kwabwera anzawo ocheza nawo, ndi kuwafunsa kuti apite kukawonera masewero a mpira kubwalo la zamasewero, iwo m'malo mongonyamuka kumapita kumasewero aja, amapita kugwada pamaso pa akzi awo, nawapempha kuti, "ndimati ndipite kukawonera masewero, ndipo akangoti ayi, basi ndiye kuti nkhaniyo yathera pomwepo, palibenso kukambirana kwina kulikonse, kapena kutsutsa kwina kuli konse kungakhalepo.

M'mene zakhaliramu ndi momwenso zimakhalira m'magawo ambiri malo a pa ntchito, komanso ku Aigupito, ndi m'mene machenjerero asatana amakhalira, powazunza ana a Heberi aja mu ukapolo asanatulutsidwe m'manja a Falao, kuti potero asathe kuwiringula kapena kudandaula kwina kuli konse.

Tikayang'ananso maiko ambiri apa dziko lino, lero zinthu zambiri zikuchitika zonyasa zimene sizifunikira kuti zizichitika pakati pa anthu, koma poti mizimu ya anthu ambiri ili yoponderezedwa ndi kuphwanyika, ambiri ngakhale aziona zoterezi salankhula kanthu, ndipo iwo ali kungozunzika osalankhula kanthu. Izitu zili kuchitika kwambiri m'maiko monga akumadzulo, ndi enanso akum'mawa ndi kumene zachulukira.

Koma tisanamalize kulongosola zambiri pa phunziro ili lopatsidwa mutu woti Mchitidwe wa Ufiti, tikufuna titambasule za ufiti di kuonanso njira zomwe tingatsate kuti tiononge mphamvu ya ufitiyi, tionanso momwe ufiti umabweretsera matemberero, pa anthu osiyanasiyana komanso mdziko, ndikuonanso njira zomwe tingagwiritsire, ntchito pofuna kuononga mzimuwu, kopanda kukhala pachiopsezo china chilli chonse kwa anthu, angakhale kwa iwo amene atenga mbali ya kuononga mizimuyi.

Mu phunziro lathu lotsatira likudzali, tidzaona m'mene ufiti ungakhale mwa munthu, ngakhale atakhala kuti iye Sanatenge nawo mbali. Tidzaona thandauzo lenileni loti ufiti, ndi chiyani, ndikutinso, ndi wofalikira motani, ndipo upezeka malo osiyanasiyana motani. Mu phunziro lathu lomaliza tidzaona mawu amene Ambuye wathu Yesu analankhula asananyamuke ulendo wobwerera kunka ku mwamba kwa Atate wake. Iye pochoka anapereka mphamvu kwa iwe ndi ine zogonjetsera mdani wathu satana. Mu phunziro limenelo tidzaonanso momwe tingagwiritsire ntchito mphamvu zimene Ambuye wathu watipatsa kuti tikathe kuononga nazo mdani wathu, mphamvu zimenezi ndi zomwe Ambuye wathu Yesu, anatipatsa kudzera pa mtanda paja, komanso tikaona chifukwa chomwe mphamvuzo sizinagwirire ntchito pa ife mwa changu.

tipezeni ife