chichewa   |   english

werengani izi

(read)

UFITI - CHOTCHINGA CHACHIKULU PA CHITSITSIMUTSO CHA MUMPINGO

(Witchcraft - the greatest barrier to revival in the church)

PHUNZIRO 3 - THANDAUZO LAKE LA UFITI M'BAIBULO
(Study 3 - The Biblical definition of Sorcery)

Mukumvetsetsa kwenikweni kwa ziphunzitso izi, panalibe cholinga china chili chonse, kufuna kuwulula anthu a mu mpingo, azitumiki a Mulungu, kapenanso othangatira kutumikira, pa ntchito ya mu mpingo, pofuna kuwapangitsa iwo kukhala ngati ochimwa pa maso pa Mulungu. Cholinga chake chenicheni cha ziphunzitsozi, nkufuna kuika pa mbalambanda mzimu wa ufiti ndi kuyamba kuonetsera m'malemba womwe ife tingagonjetsere satana mdani wathu kupyolera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Chikhalidwe cha chachitatu cha ufiti kupyolera mu ziphunzitsozi, chidzadabwitsa anthu, ichi ndi machitidwe a mtundu wamatsenga. Chikhalidwechi chimadzionetsera, chokha mu njira yomwe anthu ena sangathe kuganizirapo kanthu. Tsiku lina lililonse anthu amawerenga manyuzipepala zomwe alemba, makamaka pa mndanda uja wa zizindikiro za nyenyezi. Izitu zimathangatira kuti munthu adziwe tsogolo lake, koma chonsechi sizikhala zoona ndi pang'ono ponse. Ili ndi bodza lalikulu komanso kutsutsana kwa kukulu pa chikhulupiriro mwa Ambuye wathu Yesu Khristu pa kotengera ndi zones zimene Ambuye wathu Yesu anatichitira ndi kutimenyera nkhondo pa mtanda paja, chocho mchitidwewu suchokera kwa Mulungu, komatu kwa satana mdiyerekeziyo.

Pali anthu ambiri amene amakhulupirira kuti kuyenda kwa nyenyezi mulengalenga kumaimira zinthu zomwe zingachitike mtsogolomo pa moyo wao. Choncho izi ngati zingakhale zoona, ndiye kuti ife sitinakawerengedwa pa maso pa Mulungu kuti tili anthu ochimwa, pakuti china chilli chonse chimene timachichita pansi pano timachichita pansi pa thambo lomwe lili ndi nyenyezi. Anthu ambiri akakhala kuti akuyenda m'matemberero amanena kuti, izi ndi zomwe ndinakula nazo kuchokera kwa makolo anga.

Ndipo ena amati izi ndiye zotsatira za nyengo yanga imene ndikuyendamo, koma kuti muonetsetse muona kuti, kulankhula konseko ndi kothawa kumvomereza kulakwa kwathu. Lamulo la Mulungu lomwe tiyenera kulimvera ngati tifuna kukhululukidwa machimo athu, ndi, "Lapani ndi kukhulupirira uthenga wabwino, limene liphatikizirapo kudzipereka ndi kuyenda mu chiyanjano ndi Ambuye wathu Yesu Khristu kupyolera m'moyo wa pemphero wa tsiku ndi tsiku, ndi kumupanga Iye Ambuye ndi mpulumutso wa moyo wako.

Ungathe kulapa pa chimene sunachite bwino, choncho ngati sutenga udindo umenewu wakumvomereza tchimo lako, ndiye kuti sungathe kukhululukidwa machimo ako, pamene ukudzipangitsabe kukhala ngati munthu wopanda uchimo, ngati kuti sunachimwe. 1 Yohane chaputala cha 1:9 itipatsa ife lonjezo lodabwitsa ngatitu titatenga udindo wa kumvomereza zolakwa zathu, kuti timuuze Ambuye wathu Yesu Khristu kuti takuchimwirani mutikhululukire zolakwa zathu, ndipo mwakutero Iye ali wokhulupirika kukhululukira zolakwa zathu ndi kutiyeretsa machimo athu onse kuchokera ku zolaka zathu zonse.

Taonani momwenso Adamu ndi Hava anakanira kutenga udindo wakumvomereza tchimo lawo, pamaso pa Mulungu kuti analakwa posamvera chifuniro cha Mulungu m'munda muja mwa Ideni, tawerengani bukhu la Genesesi chaputala cha 3:8-14. "Ndipo kenaka tiwerenga kuti mwamunayo ndi mkazi wake, anamva mawu a Mulungu akulankhula nawo m'mene Iye amayendayenda m'mundamo cha kumadzulo, ndipo iwo anabisala kumubisala Mulungu mkatikati mwa masamba a mitengo ya m'mundamo. Koma Mulungu Atate anayitana mwamunayo, nati kwa iye, "Kodi ulikuti?". Ndipo iye anayankha nati ndinakumvani Inu mulikuyendayenda m'mundamo, ndinaopa chifukwa ndinali wamaliseche; chocho ndinabisala ine". Ndipo Ambuye anati, anakuuza iwe kuti uliwamaliseche ndani?. Kodi wadya chipatso cha mumtengo umene ndinakulamulirani kuti musadzadye chipatso chake?. " Mwamunayo anayankha nati, "Mkazi munandipatsa uja, anandipatsa chipatso cha m'mundamo, ndipo ndinadya icho. " Ndipo Ambuye Mulungu anati kwa mkaziyo, "Kodi ichi ndi chiyani wachitachi?". Ndipo mkaziyo anati, " Njokayo inandinyenga ine, ndipo ndinadya chipatsocho. M'malo momvomereza kulakwa kwao anakuchita, iwo anfuna kudziphimba okha kukhala ngati sanalakwe, natchula wina pa tchimo lawo, kuti potero asakhudzidwe kuti achimwa onse pamaso pa Mulungu. Kodi izi sizimene anthu akuchita masiku ano?. Sauli anafuna kukondweretsa anthu, kuti akatchulidwe kuti ndi mfumu yotchuka ya Israeli, koma iye pakufuna kukondweretsa anthu pamenepo amadzipangitsa yekha kukhala mdani wa Mulungu.

Samueli anati kwa Sauli, "Ine ndi amene Ambuye amutuma kuti ndidzakudzodze iwe, kukhala mfumu ya ana a Israeli; koma tsopano mvetsera uthenga umene ndatenga kwa Mulungu. Izi ndi zimene Ambuye akulankhula: "Ndidzalanga Amaleki, pachinthu choipa chimene anachitira Israeli, pamene Amaleki anayimitsa (waylaid), Israeli ndi kuchita naye nkhondo pamene Israeli anali paulendo wochokera mdziko la Aigupito kumuka ku dziko la malonjezano.

Tsopano muka kachite nkhondo ndi Amaleki ndi kumuononga yense kuti atheretu, ndi kusasiya kena kalikonse kamene kali ka Amaleki; iphani amuna ndi akazi onse, ana ang'onoang'ono, ndi makanda, ng'ombe ndi nkhosa zawo zonse, ngamila, ndi abulu awo onse". Choncho Sauli anaitanitsa amuna onse nawasonkhanitsa pamodzi ku mudzi wa Telamu-nawerenga kukhala 200, 000, asilikali ankhondo oyenda pansi kukachita nkhondo, ndi 10, 000 asilikali ochokera ku Yuda. Ndipo Sauli ananyamuka iye pamodzi ndi gulu la nkhondo kumuka kwa Amaleki kukachita chiwembu kudzera njira ya pansi muchingalande chakuya(ravine).

Ndipo iye anati kwa Kenani, "Chokani msanga thawani, musiye Amaleki yekha kuti ndingakuonongeni pamodzi ndi iye; pakuti inu munaonetsa Israeli zinthu zabwino pamene Iye anali kutuluka kuchokera ku dziko la Aigupito". Choncho Akanani anachoka nasiya Amaleki yekha. Ndipo kunali kuti Sauli anakantha Amaleki onse kuchokera ku Havila kufika ku Ashuri, kufikira malire ndi chipata holowera ku Aigupito. Ndipo Sauli anagwira Agagi mfumu ya Amaleki wamoyo, ndi anthu ake onse anawaononga kutheratu ndi lupanga.

Koma Sauli ndi ankhndo ache anasunga Agagi osamupha ndi nkhosa zake pamodzi ndi ng'ombe zonenepa bwino, ana ang'ombe ndi ankhosa amafuta, ndi chili chonse chimene chinali chabwino m'maso mwake Sauli. Zinthu izi sanafune kuziononga, koma zonse zinali zachabe m'maso mwake anaziononga". Ndiponso m'malo moti amvomereze kulakwa kwache, Sauli anayamba kuchita zinthu zozemba ndi kuzungulirazungulira pamodzimodzi, ndi kumanena kuti panalibe cholakwika china chilichonse, ndikumati zolinga zake zonse zinali zomvomerezeka. Komatu chimene tingadziwe ana a Mulungu ndi chakuti, ngati tipanga ubwenzi ndi dziko lapansi lino, tidziwenso kuti mwakutero tichita udani ndi Mulungu Atate.

Sungathe kusangalatsa Mulungu ndi munthu nthawi imodzi, nzosatheka zimenezo, ndibwino kusankha chinthu chimodzi, kuti ndi ndani pakati pa Mulungu ndi munthu amene ungathe kumusangalatsa. Ukamafuna kusanduliza malingaliro anthu pansi pano mokomera iwe mwini, ndinso mwakutero nupanga udani ndi Mulungu, pamenepo ugwidwa ndi machitidwe a ufiti, amene atchulidwa kale muziphunzitso zina zomwe zatchulidwa kale m'mbuyomu. Ngati munthu wafika posemphana ndi Mulungu, palibe kanthu ndiwe wochenjera motani, koma ngati walakwira chifuniro cha Mulungu, pamenepo ndiye kuti wachimwa ndithu. Patsogolo pake Sauli anachita zinthu zambiri zoyipa pa maso pa Mulungu zomwe zinatsimikizira kuti Sauli wachoka pamaso pa Mulungu, ndi kumuukira Mulungu. Pakuti chinthu china choyipa chimene Sauli anachichita ndi kufuna kuchotsa moyo wa munthu wodzodzedwa ndi Mulungu, kuti akatsogolere anthu a Mulungu, nafuna kupha Davide. Mulungu analamulira anthu ake kudzera mwa Mose. Iwo mwachidziwikire analamulidwa kuti asakayende moyo wopanda moyo wachigonjetso.

Bukhu la 1 Samueli chaputala cha 28:3-23, tiwerenga pamene Sauli anayambira kusemphana ndi chifuniro cha Mulungu, kenako anapanga zinthu zoti kwa iye maganizo anali nawo ndi oti, zinthu zomwe iye amachita zinali zinthu zabwino pamaso pake, tsopano apa tionanso kuti Samueli atamwalira, anthu onse a Israeli anamulira ndipo anthu onse a Israeli analira kumulira Samueli, nayika thupi lake m'manda mudzi wa kwao wa Ku Rama. Pa nthawiyo nkuti Sauli atayingitsa anthu onse ochita mauneneri onyeng ndi openduza pomvera mizimu yakufa, m'mudzimo. Ndiye pamene Afilisiti anamsonkhanira namanga misasa yawo ku Shunemu, naye Sauli anali kusonkhanitsa asilikali ake ankhondo, namanga misasa ya nkhondo kuGiliboa.

Ndipo pamene Sauli anona khamu la nkhondo la Afilisiti, linamchititsa mantha, nanthunthumira kuopsedwa kwakukulu mu mtima mwake. Anafunsira kwa Yehova Mulungu, kuti amuthandize kugonjetsa asilikali a Afilisiti aja, koma Mulungu sanamuyankhe, kapenanso kudzera m'maloto, ndi aneneri. Ndipo Sauli anati kwa anyamata ake omthandizira, kunkhondoko, mundipezere ine munthu wa mkazi amene ali owombedza maula, kuti ndipite ndikumane naye, ndikufunsira kwa iye za nkhondo yagwa pakati pathuyi. "Ndipo anati m'modziwa anyamata ake, pali wina owombedza maula kuEndori", iwo anatero. Choncho Sauli anazidzimbayitsa yekha pamaso pa anthu, namvala zovala zina zobisa nkhope yake, ndipo pakati pa usiku iye ndi amuna ena ananyamuka kupita ku Endori, kukakumana ndi munthu wa mkaziyi, wowombedza mawulayo, nati kwa iye, ndifunsire mzimu waulawo, "iye anatero, ndikundibweretsera ine munthu amene ndidzamtchula iye kwa iwe".

Koma mkaziyo anati, "ndithu inu mudziwa choyipa chomwe chimene Sauli anachichita". Iye anathamangitsa anthu onse owombedza mawula ndi openduza mdziko lino. Ndichifukwa chiyani munditchera msampha kuti ndikodwe, nawo ndi kuti angandiphe ine, ?. Ndipo Sauli anamulumbirira iye pamaso pa Mulungu, "ndinenetsa pamaso pa Mulungu amene alipo ndi moyo, iwe sudzalangidwa pa chinthu ichi, ndipo mkaziyo anafunsa, "kodi mufuna ndikubweretsereni ndani?. "Mundibweretsere ine Samueli". natero.

Ndipo pamene mkaziyo anaona Samueli, anadzidzimuka nakuwa ndi kulira, nati kwa Sauli, Chifukwa chiyani mwabwera ndi kundinyenga ine?. Kodi inu sindiye Sauli?, ndipo mfumu inati kwa iye, osaopa. Kodi waona chiyani?,. Ndipo mkaziyo anati, ndiona mzukwa ukutuluka kuchokera kumanda". Kodi iye awoneka ngati ndani?, anamfusa, munthu wokalamba wamvala mwinjiro, alinkukwera nkutuluka. Iye anatero.

Ndipo Sauli anadziwa kuti munthuyo, anamuonayo anali Samueli, ndipo iye analambira nagona chafufumimba(prostrate), nagwa nkhope yake pansi. Ndipo Samueli anati kwa Sauli, bwanji ukundivutitsa ine ndikumandibweretsa ine?. Pepani mbuye wanga, ndili m'mbvuto akulu" natero, Sauli. Afilisiti, anditulukira kumenyana nane ndipo Mulungu wandichokera ine, sakundiyankha kulira kwanga, angakhale kudzera mwa aneneri, kapena m'maloto, Choncho ndichifukwa ndayitanira pa inu mbuye wanga kuti mundiuze chochita". Ndipo Samueli anati kwa Sauli, "ndichifukwa ninji ukufuna ine, pamene ukudziwa kuti Yehova Mulungu wakuchokera ndi kuti wakhala mdani wako?. Mulungu wachita zomwe Iye analankhuliratu kudzera mwa ine, pakuti Yehova wang'amba ufumu wako m'manja mwako ndipo waupereka kwa m'modzi a abale ako, ndiye Davide. Izi zili chonchi chifukwa sunafune kumvera malamulo a Mulungu, ndikuwononga Amaleki kotheratu, ndipo ichi ndi chimene Yehova Mulungu wachichita ichi lero pamaso pako. Ambuye Mulungu akuperekani, m'manja mwa adani anu Afilisiti iwe pamodzi ndi Israeli, ndipo m'mawa iwe pamodzi ndi ana ako mudzakhala kuno limodzi ndi ine.

Ambuye Mulungu adzaperekanso khamu lonse la nkhondo la Israeli m'manja mwa Afilisiti. Ndipo Sauli atamva izi anagona yense wamtunthu pansi pa bwalo, ndikudzadzidwa ndi mantha kamba ka zomwe Samueli analankhula naye. Mphamvu zake zinamuthera, pakuti sanathenso kudya kanthu tsiku limenero, angakhalenso usiku wake sanadye kanthu. Pamene mkaziyo anadza kwa Sauli ndikumuona ali chigonere wonthunthumira adani ake, anati kwa Sauli, "Taona kapolo wako wakumvera iwe".

Muona kuti zotsatira za kusamvera kwa Sauli pamaso pa Mulungu zinali imfa; chigamulo cha uchimo sichinasinthe kufikira lero. Ukamapanga zinthu zomwe zingakutengere ku imfa, dziwa kuti imfa idzagwera pa moyo wako, imfa ya chiwiri yomwe ndi kuponyedwa munyanja ya moto, yomwe bukhu la Chibvumbulutso (Revelation), likulongosola bwino. Madera ambiri padziko lino, anthu ambiri amalongosola za mbiri ya makolo awo amene anamwalira m'mbuyomu, komanso mu zipembedzo zina zinthu ngati izi zimachitika kuti anthu ambiri amakhala, akupempha mizimu ya makolo awo amene anamwalira kale makamaka pakagwa bvuto pa moyo wao.

Zoterezi pamaso pa Mulungu zimakhala tchimo lomwe ndi kupembedza ufiti ndi nyanga, pakuti izi zimatithangatira kuchita zinthu zomwe ife taletsedwa kale kudzichita ndi Mulungu wathu. Tiyenera kuma kumazindikira tsogolo lathu pogwiritsa ntchito Mzimu wa Mulungu yekha amene amatiululira zinsisi za Atate wathu Mulungu, ngati Mulungu wafuna kuti ife tidziwe za tsogolo lathu, ndi Iye mwini angapereke njira kwa ife kuti tithe kudziwa tsogolo lathu, ndipo kungokambapo, tionanso kuti pali zinthu zambiri zomwe Mulungu watiululira ife ngati ana ake kuti tikafe podziwa zinthu zina ndi zina zomwe zili zotipindulira pa miyoyo yathu ya tsiku ndi tsiku, ndi kuti ife tipindule nalo baibulo lomwe liri mawu a Mulungu.

Pano pali chinthu china chake chodabwitsa, chomwe ambiri a inu mukhonza kudabwa nacho. Bukhu la Deuterenomo chaputala cha 7, chikupereka malonjezano ambiri a Mulungu pa zomwe zidza chitike pa moyo wanu ngati inu mutakhala moyo womvera Mulungu Atate wanu, angakhale kuti malonjezowa mbali imodzi ndi ya ana a Israeli, mu nthawi yake malonjezo awa adzakwaniritsidwa pa ife limodzi limodzi, tikamumvera mulungu Atate wathu kuyambira pano, kufikira mtsogolomo.

"Kondani Mulungu Atate wanu ndukusunga, mawu ake, malamulo ake, ndi zonse zimene atilamulira nazo. Kumbukirani lero kuti ana anu si amene anaona ndi kuzindikira chidzudzulo cha Yehova, Mulungu wanu; ukulu wake, mkono wake wa mphamvu, mkono wake wotambasuka, zizindikiro zodabwitsa anadzichita mkatikati mwa dziko la Aigupito, Falao pamodzi ndi anthu ake onse, zomwe Iye anachitira gulu lonse la nkhondo, la Aigupito, pa magaleta ake onse, ndi apakavalo onse, momwe Iye anawamizira m'madzi a nyanja yofiira, pamene iwo ankawalondola ana a Israeli, ndi mmwenso Mulungu anawaonongera ana a Aigupito.

Si ana anu amene anaona zimene Mulungu anakuchitirani, mu chipululu muja kufikira munafika pa malo ano, ndinso zomwe anachita kwa Datani ndi Abiramu ozikwezawo, ana a Eliabu, afuko la Rubeni, pamene nthaka inang'ambika ndi kuwameza onse pamaso pa ana Israeli onse, ndi zonse anali nazo, katundu wao, komanso ndi inu munaona ndi maso anu zinthu zonse zazikulu zimene Mulungu anachita pamaso panu inu mukuona.

Yang'anirani ndi kusunga malamulo onse amene ndi kukupatsani lerowa, choncho ndikuti mukhale amphamvu pakulowa mdziko la malonjezano ndi kuoloka Yorodano, kukalilandira dzikolo, ndi kuti mukhalitse ndi moyo mdziko limene Mulungu wanu analumbirira makolo anu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.

Dziko limene mulowamo kulilandira silili monga dziko la Aigupito, limene inu muchokeremo, kumene inu mumadzala mbewu zanu ndi kumathirira mukuyenda ndi miyendo yanu, monga m'munda wa ndiwo za masamba. Koma dziko lomwe inu muwoloka Yorodano, kukalilandira, ndi dziko la mapiri ndi zigwa limene limamwa madzi ake kuchokera kumwamba. Ndi dziko limene Ambuye Mulungu wanu amalisamalira, pakuti maso a Mulungu Atate wanu ali pa ilo nthawi zones, kuyambira tsiku loyamba la chaka chake kufikira tsiku lomaliza.

Choncho ngati inu mukhulupirika pamaso pa Mulungu wanu, ndi kusunga malamulo onse ndi kupatsani lerowa- kumukonda Ambuye Mulungu wanu, ndi kumutumikira Iye ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndipo ndidzatumiza mvula mu dziko lanu mu nthawi yabwino, kuyambira muchirimwe ndi madzinja anyengo zones, kotero kuti muthe inu kukolola zochuluka, vinyo wa tsopano, ndi olive. Ndidzaperekanso udzu wokwanira ku minda yanu wodyetsera ziweto zanu, ndipo mdzadya nimukondwera.

Khalani osamalitsa ndi kuti musanyengeke ndi kuyiwala Yehova Mulungu wanu ndi kutembenukira kwa milungu yina. Ngati mudzatero dziwani kuti mkwiyo wa Yehova Mulungu wanu, udzatsikira pa inu nonse akuchita kusaweruzika, ndipo Iye adzatseka mazenera a m'mwamba kuti mvula isagwenso, ndi kuti nthaka yanu isabalenso zipatso zake, ndipo mudzaonongeka pakuti yehova Mulungu wanu adzachotsa nthaka yanu ya bwino nimudzaonongeka. Sunganitu mawu amene ndalankhula nanu m'mitima yanu ndi m'malingaliro anu, tadziwamangani pa mkono wanu monga chizindikiro, ndins pa mphumi panu.

Phunzitsaninso ana anu malamulowa, ndi kulankhula nawo nthawi ili yonse pamene mwakhala pa nyumba zanu, pamene muyenda pa msewu, pamene mugona ndi pamene mudzuka kukacha m'mawa, kuti pakutero masiku anu ndi masiku a ana anu achuluke mdziko lomwe inu mukhala, limene Ambuye Yehova Mulungu wanu analumbirira makolo anu.

Ngati mukhala osamalitsa malamulo amene ine ndi kupatsani lerowa ndi kuwatsata-kumkonda Mulungu Atate wanu wa kumwamba, kuyenda mukumvera Iye, ndikuwasunga malamulo ake mwachangu-ndipo Mulungu Yehova adzayingitsa mitundu yonse ya anthu yomwe ya kuzungulirani, ndipo mudzawathamangitsa iwo malo awo onse amene akhalamo ndikuti inu mudzatenga dziko lalikulu pakati panu, ndipo mudzakhala mtundu wa anthu wa mphamvu.

Malo onse amene mudzaponda phanzi lanu, dziwani kuti malowo ndakupatsani kukhala anu. Malo anu okhalamo adzakulitsidwa kuchokera ku chipululu kufikira kumalekezero aLebano, ndi kuchokera ku tsinje waFirate ndi kukafika ku Nyanja ya Mediteraniyani. Palibe amene adzatha kuyima ndi kukutsutsani. Yehova Mulungu wanu, monga Iye analonjeza inu, adzaika mantha ndi chiopsezo pa mitundu yonse yokuzungulirani inu, ndi kuli konse mudzapitako. Zindikirani chinthu ichi kuti Yehova Mulungu wanu walonjeza mvula mu nthawi ya bwino ndi kukhala pa mtendere opanda nthenda ina ili yonse. Mankhwala sikuti ndi olakwika, paokha, koma kupita kwa asing'anga kukakuphatikizirani zitsamba ndi kuti muchire, dziwani kuti zoterezi ndizo tikudzitcha kuti ufiti ndi nyanga. Madera ena a dziko la pansili ndi kudziko la Indiya, nyengo ya mvula nthawi zina imakhala yochedwerapo, ndipo nthawi zina imatha kulephereka osabwera mvula nyengo yonse. Lero anthu oyang'ana zinthu za Sayansi, akumatha kuwulutsa ndege zawo kupita m'mwamba kufikira mtunda wokwanira, 30, 000 fiti, ndi kumapopera mankhwala mulengalenga ndi cholinga choti mvula iyambe kugwa.

Zoterezinso ndi zija tikudzitcha kuti kupembedza nyanga ndi ufiti womwe. Ngati uli nayo nthawi ndipo ukufuna kuti mvula mdziko lako iyambe kugwa tayamba kuchita zinthu ngati zimene anachita Eliya, mu bukhu la 1 Mafumu chaputala cha 18:41-46, tawerengani pamenepo. Eliya anati kwa Ahabu mfumu, "pitani kadyeni ndi kumwa pakuti kukumveka mkokomo wa mphamvu wa mvula yaikulu kuti ili nkudza". Choncho Ahabu ananyamuka nakamwa ndi kudya. Koma Eliya anakwera kunka kuphiri la Kalimeri, napinda maondo ake pansi natenga nkhope yake nayika pakati pa maondo ake. "Pita nuyang'ane mbali mwa Nyanja, anatero kwa mnyamata wake, iye napita kukaona. Ndipo anati kwa mbuye wache, palibe china chili chonse, anatero. Kasanu ndi kawiri Eliya anatero naye mnyamata wake, nati bwerera kayang'ane.

Ndipo kachinayi ndi chiwiri, mnyamatayo anati kwa Eliya, taonani kamtambo kakang'ono kokhala ngati dzanja la munthu kakutuluka kuchokera mnyanja". Choncho Eliya anati, "pita kamuze Ahabu, kuti manga zingwe za galeta wako nunyamuke chifukwa mvula ya mphamvu ingakutsekerezeni, ndipo pa nthawiyo kumwamba kunada kuti bi!, ndi mitambo ya mvula, ndipo mphepo inawomba ya mvula, ndipo mvula ya mphamvu inayamba kugwa nathamanga Ahabu, pa galeta wake kulunjika ku chipata cha Yezireeli. Ndipo mphamvu ya Mulungu inatsikira pa Eliya, napisira chovala chake mlamba la mchiunu mwache, nafulumira patsogolo pa Ahabu kuthamangira ku chipata cha Yezireeli!.

Njira yopewera chilala cha kusowa madzi, ndi njiranso ya kubooeza ndiyo kukhala m'moyo wakumvera Mulungu, ndi kuwapanganso anthu kukhala omvera Mulungu ndikuthandizadziko kuyenda pamaso pa Mulungu, wamoyo amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi. Lero ngati dziko likudutsa mu nyengo yachilala, chosowa madzi, dziko likuyenera kufuulira pamaso pa Mulungu anthu onse pamodzi, kapena apo ayi anthu angapo oyimirira maiko awo apemphere kupempherera dziko lawo. Njira ina ili yonse yopembedza zinthu za matsenga ndi za ufiti zimangotibweretsera mabvuto pakati pathu. Musamatemberere munthu wina ali yense, komanso musalole kumvomereza themberero kuchokera kwina kuli konse. Mudzisamala chifukwa nthawi zina mawu amkamwa mwanu, amene ali odzetsa matemberero pakati panu, muyenera kumakaniza mawu ali wonse amatemberero, pa moyo wanu. Ngati muona kuti mwa phwanya mphamvu yonse ya matemberero dziwani kuti zidzatero monga ndi mawu amkamwa mwanu. Phunziro lomaliza, limene lili phunziro 4. Likuonetserani momwe mungathere kuwononga ndi kugonjetsa mphamvu ya ufiti, ndinso momwe mungagonjetsere ufiti mdziko lanu, ngakhale kwina kuli konse kumene mungapite. Musanayambe kuwerenga phunziro lotsatiralo, yambani mwa werenga kaye bukhu la Deutereronochaputalacha7, chifukwandichaputalachofunika kwambiri ndipo chikhonza kukhala mdalitso waukulu pochita zinthu zomwe tikhale tikudziona mu phunziro 4 likudzali.

tipezeni ife