chichewa   |   english

werengani izi

(read)

UFITI - CHOTCHINGA CHACHIKULU PA CHITSITSIMUTSO CHA MUMPINGO

(Witchcraft - the greatest barrier to revival in the church)

PHUNZIRO 4 - KUPHWANYA MZIMU WA UFITI
(Study 4 - Breaking the spell)

Mukumvetsetsa kwenikweni kwa ziphunzitso izi, panalibe cholinga china chili chonse kufuna kuwulula anthu amene a mumpingo, azitumiki a Mulungu kapenanso kuwapangitsa iwo kukhala ngati ochimwa pamaso pa Mulungu. Cholinga chake chenicheni cha ziphunzitsozi nkufuna kuika pa mbalambanda mzimu wa ufiti ndikuyamba kuwonetsera m'malemba, momwe ife tingagonjetsere satana mdani wathu kupyolera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Mu bukhu la Hoseya chaputala cha 4:6, tili ndi mawu odziwika bwino amene tinafika poloweza pa mtima, "omwe amati, anthu anga akuonongeka kamba kakusadziwa". Mdaniyo amafunitsitsa kukupangitsani kuti mudziona ngati anthu opanda mphamvu kuti simungathe kumugonjetsa, koma podziwa inu zonse zimene Ambuye wathu Yesu Khristu anachita pokwaniritsa zinthu zonse, pa inu kukumenyerani nkhondo pa mtanda paja. Tawerengani tsono ma vesi omwe akuchokera m'bukhu la Aefeso ma chaputala awa: 1, 2 ndi 4.

"Mayamiko ndi matamando akhale kwa Mulungu Atate wa Ambuye wathu Yesu, amene atidalitsa tonse ndi madalitso onse a azam'mwamba, ndinso ndi madalitso a uzimu mwa Khristu Yesu. Anatisankha ife tonse mwa Iye mwini lisanakhale dziko lapansi, kukakhala oyera mtima ndi opanda banga pa maso pake. Kupyolera mwa chikondi chake Iye anatipangiratu kutitenga kukhala ana ake, kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, monga kunamkomera Iye ndi chifuniro chake- kufikira kuchitira dzina lake matamando ndi mayamiko, muchisomo cha ulemerero wake, chimene chapatsidya kwa ife mwa Iye amene amkonda. Ndipo mwa Iye tili ndi chipulumutso kudzera mu mwazi wake, kukhululukidwa kwa machismo athu, monga mwakuchuluka kwa chuma cha Mulungu ndi chisomo chake chimene anachisiya pa ife.

"Koma monga inu munali akufa, munali akufa kudzera mu zolakwa zanu ndi uchimo wanu, umene munakhalamo, potsatira njira zoyipa za dziko lino, ndi kutsatira zolakwa za mkulu wamdima wa za m'mwamba, mzimu womwe ukugwira ntchito mwa iwo akukhala moyo wosamvera Mulungu. Komatu ife tonse tinakhala pakati pawo, ndikukondweretsa chilakolako cha thupi. Monga mwa kuchimwa kwathu, tinayenera mwachikonzero cha Mulungu kukhala anthu olawa mkwiyo wake ndiyo imfa yodza kamba ka uchimo.

Koma kamba ka chikondi chake chachikulu pa ife, Mulungu amene ali wolemera muzifundo, zake, anatipanga ife tikhale ndi moyo, ngakhale kuti tinali woperewera mu ulemerero, wake-choncho ndife opulumutsidwa ndi chisomo chake. Mulungu anatiukitsa pamodzi ndi Yesu Ambuye wathu, ndikutikhazika mu ulemerero wake wa m'mwamba mwa Yesu Khristu Ambuye wathu, ndicholinga choti mu nthawi ilinkudzayo, akatiwonetsere ife chuma chake chosasimbika cha chisomo chake, cholongosoledwa mwa kukoma mtima kwake mwa Yesu Ambuye wathu. Ndi mwachisomo cha Mulungu kuti inu munapulumutsidwa, kudzeratu mu chikhulupiriro-ndipo izi sizinachitike chifukwa cha inu nokha, komatu ndi mphatso ya Mulungu kuti pasakhale wina wa inu odzitamandira. Ife ndife zipangizo zake za Mulungu, wolengedwa mwa Khristu Ambuye wathu Yesu kukachita ntchito za bwino, zimene Atate Mulungu anazikonzeratu, kuyambira pa chiyambi zinthu zonse zisanalengedwe kuti ife tikadzichite. Choncho kupyolera mu mavesi ochepawa, taphunzira kuti ife tinalandira chikhululukiro cha machimo athu, kupyolera mu kukhetsedwa kwa mwazi wake wa Yesu Ambuye wathu pamtanda paja, choncho tsopano ife tili kulamulira nawo pamdzi ndi Iye Ambuye wathuYesu mu zinthu zones za m'mwamba.

Sipokhaponso ayi, izi ndi zina zochepa za zimene Ambuye wathu Yesu Khristu anatichitira kutipambanitsa tonsefe, pa mtanda paja. Nanga ndi chifukwa chiyani akhristu ambiri lero kuyenda m'moyo wopanda mphamvu? Zili chomwechi chifukwa iwo sanalowe moyo wonse wa zimene Ambuye wathu Yesu Khristu anatichitira pa mtanda paja. Chifukwa cha zonsezi, ndi chakuti pali munthu anatha kuwalongosolera za chigonjetso cha Khristu Yesu chimene anachichita pa mtanda paja. Ambiri sanayambebe kuphunzitsa mitu ya ziphunzitso ngati izi, chifukwa cha mantha kuti, kodi tikayamba kuwaphunzitsa anthuwa ziphunzitso za mtunduwu anthu, kodi ndiye kuti ife zitithera bwanji, ngati atatero.

Maganizo amtundu woterewa ndi amene amachitika ndi machitidwe a ufiti, mantha omuchitira mdani wathu, amene ife makamaka, tili ndi ulamuliro wa mphamvu pa iye mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. Bukhu la Luka chaputala cha 10:19-20, ilongosola za Yesu m'mawu ake kunena ndi ophunzira ake kuti, pa nthawi yomwe iwo ankachokera kukatumikira atawatuma opanda Iye mwini.

"Ndakupatsani mphamvu ndi ulamuliro wa kuponda pa njoka ndi zinkhanira kuti mukagonjetse mphamvu yonse ya mdani wathuyo, ndipo kuti palibe chilli chonse chokukupwetekani. Koma tsono musakondwere kwambiri kuti mizimu inakugonjerani, koma kuti mukondwere ngati mayina anu alembedwa m'mwamba. Mu vesi ya 28 ya bukhu la Mateyu chaputala cha 10, Yesu analankhula ndi ophunzira ake kuti, "ndakupatsani ulamuliro ndi mphamvu ya kuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi kugonjetsa mphamvu zones za mdani wathu;ndikuti palibe chokupwetekani inu.

Koma tsono, musakondwere kuti mizimu inakugonjerani ndi kukumverani inu, koma kondwerani kuti mayina anu alembedwa m'mwamba. Kodi inu munaonapo munthu wina utumiki wa mamasulidwe utamuchitikira? Nthawi zina pamakhala kukuwa ndi kujowa m'mwamba ndi chisangalalo. Kodi mukudziwa chifukwa chake? Chifukwa ndi chakuti munthu wina aliyense amene akudziwa za ulamuliro umene ulu mwa Khristu Yesu, adzakhala munthu amene satana nthawi zones adzachita naye mantha.

Koma wina akadzafika poyamba kuphunzitsa ziphunzitso izi, ndi kuona Mulungu akumasula anthu ochuluka, mu mphamvu ya ufiti, ndi zotsatira za matemberero, iwo sadzafunanso kukabwerera kumakaphunzitsa ziphunzitso zinanso. Pamene pachitika mulandu womwe munthu wina wa palamula, chinthu choyamba chimene apolisi amayamba kuchifufuza ndi kufuna kudziwa kuti chigawengacho chinalowera pati popita kukathyola nyumbayo, momwenso ndi mene zimakhalira ndi ufiti, pamene ife tadzwa kuti ufitiwo unalowa motere timayamba kupeza njira zoutulutsira ufitiwo.

Izitu sizodabwitsa kuona kuti akhristu ambiri lero akuyenda m'matemberero amakolo awo, amene sanathyokepo. Aliyense amene ali wokhulupirira ndi munthu woti ndiwokhudzidwa ndi miyambo ya makolo. Matemberero amakolo ndi matemberero oyenda kuchokera mukupatsirana kuchoka pa m'bado wina kufikanso m'bado wina.

Tingoyang'anapo momwe nthawi zina zimene anthu amanena, kuti ziwanda zakumwa, zoona zake ndi izi, ngati mwina m'modzi wa makolo ako anali ndi mzimu woledzera, ndiye zinthu ngati izi zimakhala zapafupi, kuti wina atengerepo. Themberero lina limene limabwera, kudzera kupatsirana kwa anthu apachibale ndilo themberero lazilakolako zathupi. Ngati bambo ako anali okonda akazi kukwatirakwatira, mzimu womweo udzayendanso pa iwe. Zinthu ngati izi zimakhala zochitika, nthawi zones, koma tiyeni tiyang'ane zinthu zomwe zisali zodziwikiratu? Chimodzi, kapena zingapo zomwe makolo anu anakhudzidwa nazo, monga kukhala ndi mizimu yolosera za mtsogolo, kapena kuti mulauli, wolosera zinthu za patsogolopo(Numakhulupirira kuti ukamawerenga mitundu ya nyenyezi zomwe umaganiza kuti zimakhala zikulongosola tsogolo la munthu), zinthu zonsezi ndi zoletsedwa m'baibulomu, chifukwa zimangokuchotsetsa choonadi cha Mulungu pamaso pake.

Kholo lako linayenera kukhudzidwa, mwanjira ya kulumikizana ndi mizimu ya anthu akufa. M'maiko ambiri pa dziko lapansili, anthu ochuluka amakhulupirira ndi kulimbikitsidwa kuti azitha kulumikizana ndi mizimu ya abale awo amene anamwalira kale kale, ena amawalimbikitsa kuti adzipembedza mizimu ya anthu oyera mtima amene anamwalira zaka zambiri zapitazo, zonsezi izi ndi zosamvomerezeka ndi mawu a Mulungu m'baibulomu ndipo zimangopangitsa udani ndi Mulungu.

Moyamika tinene kuti Mulungu, watilonjeza ife kuti ngati tingatsatire njira zake ndi kuyenda muchiyanjano ndi Iye, ndiye kuti adzatsegula makomo a madalitso athu ndikutipulumutsa kuzinthu zones zoyipa. Lonjezo zodabwitsa kuwonjezera apa ndi likupezeka mukalata woyamba wa mtumwi Yohane chaputala cha 1:9, imene tiwerenga kuti, "Ngati timvomereza machimo athu, aliwokhulupirika ndi wolungama kutikhululukira zolakwa zathu, ndikutiyeretsa zolakwa zathu.

Pakutha pa maphunzirowa, mudzapeza mtundu wa mapemphero, womwe adzatha kumasula anthu, kumasulanso mzinda umene mukhalamo ndi anthu amtundu wonse okhala nawo amene anatha kumangidwa ndi mizimu yoipa ndi matemberero a mtundu wa ufiti. Zimenezi zimakhala zikugwira ntchito m'magawo onse atatu, monga zakhala zikuoneka zikuchitika nthawi yosawerengeka, ndiye mukhonza kugwiritsa ntchito mapembedzero ndi mapemphero, pakuti mapemphero ayenera kukhazikika pa malemba chifukwa izi ndizimene baibulo likulongosola.

Chimodzi mwa zinthu zosaoneka ndi maso awanthu zomwe ndi mchitidwe wa ufiti, ndi monga zomwe limachitaboma, ndi azasayansi pa nthawi yoti mvula yasowa mdziko. Iwo amapopera mpweya wamakemiko kupititsa mulengalenga kuti mvula iyambe kugwa, awa ndi matsenga a ufiti chifukwa malonjezano a Mulungu mu bukhu la Levitiko chaputala cha 26:4, Mulungu akulonjeza kuti ngati mudzamvera malamulo ake ndikuyenda mu njira zake zones, ndipo ndiye kuti Mulungu adzakupatsani mvula yabwino mu nthawi yake.

Kodi zoyenera kuchita ndiye ziti pamene mvula yavuta mdziko lanu? Muyenera kuchita moyenera monga anachita Eliya pamene mvula inasowa mdzikomo, kwa zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umdzi. Mu bukhu la 1 Mafumu chaputala, 18:41-46 tiwerenga, kuti: Eliya anati kwa Ahabu, pitani, kamweni ndi kudya, pakuti kukumveka mkokomo wa mphamvu wa mvula, choncho Ahabu anathamanga nafulumira kukadya ndi kukamwa, koma Eliya anakwera mphiri la Kalimeri, nagwa nkhope pamaso pa Mulungu naika nkhope yake pakati pa mawondo.

"Pita kayang'ane kunyanja, anatero kwa mnyamata wake, womtumikira". Ndipo iye anapita nakayang'ana nati, Palibe chomwe chiliko", anatero. Kasanu ndi kawiri Eliya anamtuma iye kukayang'ana, nati kwa iye bwerera kayang'anenso, napita iye ndipo kachisanu ndi chiwiri anati, "ndiona kamtambo ngati dzanja la munthu kalikukutuluka mnyanjamo, choncho Eliya anati, thamanga kamuuze Ahabu kuti amange galeta wake, nathawe chifukwa mvula ya mkokomo ingamutsekereze iye panjira. Posakhalitsa kumwamba kunada kuti bi! Ndi mtambo wa mvula yaikulu, mphepo inaomba ndipo mvula ya mphamvu inayamba kugwa, ndipo Ahabu anathamanga kuthawa mvulayo kulowera ku chipata cha Yezereli. Ndipo mphamvu ya Mulungu inadza pa Eliya namanga lamba mchuuno mwake nathamanga patsogolo pa Ahabu kulowera ku chipata cha Yezereli. Mphamvu ya Mulungu inagwira ntchito pa Eliya, chodziwika ndi chakuti Mulungu sanasinthe akadali yemweyo, zodabwitsazinso zidzatha kugwira ntchito pa inu lero, ngati mungathe kutsatira moyo wa pemphero limene likhonza kuononga mphamvu ya ufiti pa moyo wa munthu.

ndikukutengerani themberero, ngati simungathe kukhala woyembekezera m'banja, anthu ena amapita kwa asing'anga kukapempha thandizo loti apeze mwana m'banja, ndipo kenaka msing'anga amakupatsani mankhwala osakanizidwasakanizidwa, ndipo ukamwa upezeka kuti m'masiku ochepa uliwoyembekezera, pamenepanso pofunika kukhala osamala chifukwa yotereyi sikhala mphatso yochokera kwa Mulungu. Nankha chofunika kuchita ndi chiyani?, tiyeni tione zowe anchita Hana ali ndi chosowa m'moyo wake, werengani bukhu la 1Samueli chaputala cha 1:1-20.

Taonani kunali munthu, wina wa kuRamatayimu wochokera dara la kumapiri a Efremu, amene dzina lake anali Elikana mwana waYerohamu mwana waElihu, mwana waTohu. Iyeyu anali ndi akazi awiri, woyamba ndiyeHana, ndipo winayo analiPenina. Ndipo anali ndi ana, koma Hana analibe ana. Chaka ndi chaka munthuyu amachokera kumudzi kwao kupita kukapembedza ndi.

Kukapereka nsembe pamaso pa Mulungu ku Silo, kumene Hofini ndi finihasi ana a Eli wa nsembeyo amagwira ntchito ngati ansembe. Ndipo nthawi ikakwana yokapereka nsembe Elikana, amatenga gawo la nyama nampatsa Penina, ndi ana ake onse amuna ndi akazi. Koma kwa Hana amapereka magawo awiri, chifukwa anali kumukonda kwambiri.

Ndiye pakuti Ambuye Mulungu anatseka mimba ya Hana, kuti asabale ndipo pamenepa mkazi mzakeyo anali kumuputa ndi kumunyoza opanda chifukwa ndi choilinga chofuna kumupsetsa mtima Hana, ndipo zoterezi zinali kuchitika chaka ndi chaka, ndipo pamene Hana akanyamuka kumuka kunyumba ya Mulungu, mkazi mzakeyo anali kumuyamba ndi kumukwiyitsa kufikira Hana sanali kudya chakudya chifukwa amakhalira kulira nthawi zones. Mwamuna wake Elikana amalankhula naye, motere :Hana, ndi chifukwa chiyani ukungolira? Bwanji osadya hakudya?, ndi chifukwa ninji ukungogwetsa nkhope yako pansi nthawi zonse?, kodi sindili oposa ana khumi kwa iwe?

Ndipo atatha kudya ndi kumwa ku Silo, Hana anayimirira. Taonani Eli wansembe analikukhala pa mpanda wake pafupi ndi khomo lolowera kukachisi. Hana mowawidwa mtima anapemphera moswka mtima kwa Mulungu, nalira mosisima, ndipo anachita pangano ndi Mulungu, nati, Ambuye Mulungu wa mphamvu yonse, mukaona kulira kwa mnzakazi wanu, ndikundikumbukira ine ndikusayiwala mnzakazi wanu, ndi kumupatsa mwana wa mwamuna, ndipo ndidzamupereka kwa Ambuye Mulungu wanga masiku onse a moyo wake, ndipo pa m'mutu mwake simudzameta lumo.

Pamene Hana anali kupempherabe pamaso pa Mulungu, Eli wansembeyo anamyang'anitsitsa pakamwa pake, koma Hana anali kupemphera cha mumtima osatulutsa mawu, koma milomo yake yokha inali kungogwedera, ndipo mawu ake sanali kumveka. Ndipo eli anaganiza kuti mkaziyo analedzera mowa, nati kwa iye, "kodi udzasiya liti kuledzera mkazi iwe? Chotsa vinyo wako pamaso pa Mulungu.

"Sichoncho, mbuye wanga, " Hana anamyankha wa nsembeyo, "ndine mkazi amene ndili wosowa mtendere m'moyo mwanga. Mowa sindinamwepo, angakhale vinyo, koma ndilikutsanulira moyo wanga pamaso pa Mulungu Ambuye. Musafanizire nzakazi wanu ndi akazi oyipa;ndinali kupemphera pno kuchokera muchisautso changa chachikulu, ndi chisoni chachikulu. Ndipo Eli anamyankha iye nati, "pita mu mtendere, ndipo Ambuye wabwinoyo wa Israeli akupatse chokhumba chako chomw wa pempha.

Ndipo Hana anati, "mnzakazi wanu apeze chisomo pamaso panu". Ndipo Hana ananyamuka napita nakadya, ndipo nkhope yake sinalinso ndi chisoni. Ndipo m'mamawa iwo anadzuka nayamba kulambira ndi kupembedza Mulungu, nanyamuka kumuka kwao kuRama. Elikana anamkonda mkazi wake namdziwa, ndipo Atate Mulungu anamkumbukira hana. Choncho munthawi yoikika ya Mulungu, Hana anali woyembekezera nabala mwana wa mwamuna. Namutcha iye Samueli, nati chifukwa ndinapempha mwanayu kwa Mulungu, ndidzampereka iye kwa Mulungu moyo wake wonse.

Momwemonso monga mungaganiziremo, kukhala m'mnyengo yobwerera m'mbuyo, kuchotsa pakati ndi tchimo lalikulu pamaso pa Mulungu, chifukwa ndi Mulungu yekha amene amapanga chiganizo pa moyo wa munthu, ngati angakhale ndi moyo kapena kufa. Koma ngati muchita nokha muchifuniro chanu kuchotsa moyo wa munthu mwa njira ya kuchotsa mimba apo tili kungochita pofuna kuputa mkwiyo wa Mulungu, zimenenso satana anachita pofuna kuyamba mkwiyo wa Mulungu, zinthu ngati izi zili pansi pa mchitidwe wa ufiti monganso mwa ziphunzitsozi.

Tsopano tiyeninso tiwone ena mwa malonjezo a Mulungu ndi machenjezo ake mu bukhu la Deuteronomo chaputala cha 7 monganso ali kufanana ndi phunziroli, ndinso tiwone kufunikira kwacha. Muchaputalachi, tiwerenga kuyambira vesi ya 1- 15:Pamene Ambuye Mulungu wanu akutulutsani mu dziko la Aigupito ndi kumuka nanu ku dziko la Kanani, ndikuyingitsa adani anu pamaso pa mitundu ya anthu. - a Hiti, Giligasi, Amoni, Kanani, Perezi, Hivi ndi a Yebusi, ngakhale mitundu ya anthu akuluakulu, ndi oposa inu-ndi pameme Mulungu wanu awapereka iwo m'manja mwanu, kuti muwagonjetse iwo, muyenera kuwaononga iwo kotheratu kuti asapezekenso pakati panu, musapangane nawo mapangano ena ali wonse ndi iwo, musawachitire chifundo, musapange nawo ubale wina uli wonse wa ukwati pakati panu ndi iwo.

Musapereke ana anu akazi kukwatirana nawo, kapena kutenga ana awo akazi ndikuwapatsa ana anu amuna kukwatiranawo, chifukwa mukatero adzatha kuwatembenuza ana anu ndi kuyamba kutsatira njira za iwo kuyamba kupembedza milungu ya kufa, ndipo mutatero dziwani kuti mkwiyo wa Mulungu Atate wanu udzagwera pa inu ndipo Mulungu adzafulumizika kukuwonongani inu. Tsono izi ndi zomwe mudzichita ndi iwo, phwanyani maguwa awo ansembe, phwanyani ndi kusaladza miyala yawo yoperekera nsembe kwa milungu yawo ya kufayo, dulani pakati tsanamira za Ashera ndikutentha mafano awo onse.

Inu ndi anthu a mwini Mulungu woyerayo, pakuti Atate wanu Mulungu anakusankhani inu, pamaso pa mitundu yonse ya padziko lino la pansikukakhala anthu ake, ndinu chuma cha mtengo wache wa patali wa Iye mwini Mulungu. Mulungu Atate wanu sanakukondeni kuti mukhale ana akke, chifukwa choti munali ochuluka kuposa mitundu ina ya anthu, pakuti inu munali ochepetsetsa mwa anthu onse a pa dziko lapansi.

Komatu chifukwa choti Mulungu Ambuye wanu anakukonda inu ndikusunga pangano analipanga ndi makolo anu, kuti adzatulutsa inu ndi mkono wake wa mphamvu, ndi kukupulumutsani inu ku dziko la ukapolo wa Aigupito kuchokera m'manja mwa Falawo mfumu ya Aigupito. Choncho dziwani inu kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu;Iye ndi Mulungu wokhulupirika nthawi zonse, wakusunga malonjezano ake kuyambira kumibado ndi kufikiranso kumibado makamaka kwa iwo akumukonda ndi kusunga malamulo ake awachitira chifundo chosatha.

Koma onse akumuda Iye adzawaononga pamodzi;koma Choncho khalani osamala kwambiri, posunga malamulo ake, ndi kuwachita. Ngati mudzafulumizika kuchita malamulowa, ndi kuwatsata, ndipo Mulungu Atate wanu adzasunga malonjezo ake onse, achikondi ndi inu monga Iye anachita malonjezo ndi makolo anu.

Yehova adakukondani ndi kukudalitsani inu nakuwonjezerani inu kuchuluka kwanu. Adzadalitsa zipatso za mthupi mwanu, mbewu ya kumunda kwanu, mbewu zanu, vinyo watsopano ndi mafuta a olive, ana a ng'mbe ndi nkhosa a zoweta zanu, ku dziko lomwe yehova analumbirira makolo anu.

Mudzakhala odala inu kuposera anthu ena onse, palibe m'modzi wa inu mwamuna kapena mkazi adzataya mwana m'mudzi mwanu, ngakhale zoweta zanu sizidzakhala zopanda ana. Mulungu wanu adzakutetezani inu ku matenda onse. Iye sadzakukanthani inu ndi nthenda yoopseza miyoyo yanu, imene munkaidziwa muli ku dziko la Aigupito. Koma Mulungu adzakantha onse ndi nthenda zoopsa akukudani inu.

Musanayambe kupemphera potengera zinthu zimene mwamvazi, choyamba valani zida zonse za Mulungu monga kwalembedwa mu bukhu la Aefeso chaputala cha 6:10 -18"Chotsiriza tadzilimbikani mwa Ambuye ndi mphamvu yake. Valani zida zonse za Mulungu, kotero kuti mukhinza kuchilimika ndi kuyima pamaso pake pokana machenjerero a mdyerekezi.

Pakuti kulimbana kwathu sikuli kwathupi ndi mwazi, koma amaulamuliro ndi olamula a mdima, ndi mphamvu ya mdima uno ndi ochita zolimbika za mlengalenga. Choncho tavalani zida zonse za Mulungu, kuti pamene tsiku loyipa likabwera mudzathe kuima ndi kuchilimika, ndipo mutatha kutero mudzachilimika.

Imani nji!, mutadzimangira lamba wanu mchuuno, ndi chapachifuwa chimene chilli chachilungamo chanu, mutadzivekanso kumapazi kwanu ndi uthenga wa mtendere. Pamwamba pa zonse dzitengereni nokha chotchinga chochilikiza mivi ya woyipayo, chimene chilli chikhulupiriro, chimene inu mudzakhonza nacho kuzima mivi yoyaka ya woyipayo.

Tenganinso chisoti chachipulumutso, ndi lupanga la Mzimu woyera limene amene ali mawu a Mulungu. Pempherani ndi Mzimu woyera nthawi zonse ndi mapembedzero onse ndi ndi zopempha pamaso pake. Mwakutero, khalaninso odziyang'anira ndi kukhala m'moyo wapemphero nthawi zonse ndi kuwapempherera anthu onse oyera mtima, pemphaninso Mulungu kuti akukuteni ndi kukuphimbani ndi mwazi wake wa Yesu, pofuna kuwonjezera chitetezo, kuletsa mphamvu iliyonseyo ya mdani wathu satana.

Zinthu izi zichitani nthawi ina ili yonse musanadzuke kapena musanachite kanthu kena kalikonse. Tsono chikakhala chizolowezi cha nthawi zonse kwa inu, ndiye kuti tsono mudzalandira mavumbulutso a Mulungu wanu nthawi zonse mwa kupemphera ndi Mzimu wake. mwakutero kudzera mpemphero la dziko lanu, kapena anthu amene mukhala nawo pafupi m'Madera mwanu potsutsana ndi matemberero. Kudzera mu pemphero la mtundu woterewu muona kuti mukhonza kuchita kafukufuku wa machimo odzera ku matemberero a makolo athu, ndikuyamba kulapa pamaso pa Mulungu kuwalapira iwo ngati kuti machimowo, tinawachita ndife. Pempheni Mulungu kukhululukira makolo athu machimo onsewa, ndinso kukhululukira ife tonse machimo athu, ndikuwabwenzera kukhala tsopano madalitso pa ife ndi anthu onse amderalo.

Bukhu la Nehemiya chaputala cha 1:5-7, tiwerenga kuti, "Ambuye, Mulungu wa kumwamba, wamkulu ndi Mulungu wolemekezeka, amene asunga malonjezano ache achikondi kwa onse amene amkonda Iye ndikusunga malamulo ake,, tcherani khutu lanu ndi maso anu apenye, ndikumvetsera pemphero la kapolo wanu limene iye apemphera pamaso panu usiku ndi masana, chifukwa cha akapolo anu ana a Israeli.

Ndikumvomereza machimo athu pamodzi ndi machimo anga amene ife tawachita, ndi nyumba ya makolo anga yakuchimwirANI Inu. Tachita chosalungama pamaso panu, sitinakhonza kumvera malamulo anu mulungu amene munamupatsa kapolo wanu Mose". Izi sizongochita munthu m'modzi yekha achite, koma ndi zofunika kuti anthu ochuluka achite.

Bukhu la Danieli chaputala cha 9, mneneri ndiye amapemphera kwa Mulungu nalapa machimo ake pamodzi ndi machimo a anthu onse, zotsatira zake tiona kuti mngelo wa Mulungu amaonekera pakati pawo, zinali kutero ndi woyimirira anthu onse akaona kuti anthu achimwa, pamene apemphera anthu amaon kuyenda kwa mkono wa Mulungu pakati pawo.

Pano pali mndandanda wa zinthu zomwe zimachititsa kuti matemberero abwere pakati pa anthu, kapenanso munzinda wokhalamo, tawerengani ndikulapa zinthu za mtundu woterewu, monga Taroti Khadi, kuwonera ndi kumvera zinthu zolawula zomwe tizitcha kuti ndi zinthu zobweretsa matemberero pa moyo wa munthu.

Kumwa mowa mwa uchidakhwa, kusakhululukira anthu ena nkumatha zaka zambiri, munthu ukusungabe zifukwa mumtima, kusuta fodya, kuyitanira pa mizimu ya anthu akufa, kapena kulumikizana ndi mizimu ya anthu akufa mwanjira ina ili, yonse, kupembedza mafano ndi milungu ya kufa, kuchita zinthu za matsenga, ndi zina zotere.

Kulambira zinthu zowumba kaya ndi zazing'ono kaya ndi zazikulu, mwachitsanzo monga mulungu wa Buda, mabukhu, magazini ndi marekodi ndi kupembedza milungu ya kumidima, kuvala zinthu zoko metsera thupi. Zinthu zoonera monga mafilimu, Masewero owonera pa kompyuta monga masewero olawula, zizindikiro za kumidima zosonyeza ziwanda, ndi zonse zooneka kuti zinthuzi ndi zaufiti, kukhala ndi moyo wansanje ndi munthu wina, kukhala m'moyo wodzitamandira, kusokondwera ndi anthu ena akachita zinthu zabwino, zonsezi tizika mgulu la machitidwe a ufiti. Pamenepa mwina nkutheka kuti ndi iwe, kapena azigogo ako, mwina makolo ako, amene, chofunika ndi kulapa kudzilapira pamaso pa Mulungu, komanso kulapira anthu ena amene ali okhunzidwa ku mphamvu ya matemberero yochokera kuzikhulupiriro zonyansa. Tsopano mutatha kulapa ndi kumvomereza machimo anu pamso pa Mulungu, mukhonza kumufunsa Mulungu Atate wanu kuti aphwanye matemberero onse amene anachitika ndi moyo wanu kuchokera kumphamvu ya kusamvera Mulungu kuti tsopano mukhale anthu omasulidwa okhala mu chiyanjano ndi Mulungu, ndipo mumfuse Mulungu kuti akhululukire zolakwa zanu, ndikuti mudziyenda m'moyo wachiyanjano ndi Iye.

Pamene mufuna pemphero logonja pamaso pa Mulungu kulapira dziko ndi mtundu wako, komanso iwe mwini wako, werengani bukhu la Danieli chaputala cha 9, ndipo mudzapeza zinthu zambiri zomwe iye anachita pofuulira pamaso pa Mulungu ndi kupereka anthu amtundu wake m'manja mwa Mulungu kuti awakhululukire zolakwa zawo. Munthawi yomwe iwe ukuyembekezera mwachikhulupiriro, kuti utatha kupempherera dziko lako Mulungu nasintha nyengo ya anthu amdzikolo, ndi pamene umafunika kukhala m'moyo woyenda pamaso pa Mulungu mokhulupirika nthawi zonse, ndikuyendanso moyo womkondweretsa Ambuye. Kumbukirani kuti mapembedzero amtundu wotere sangangosintha nyengo ya dziko lako, nthawi imodzi, komatu ukamapitiriza kumupempha Ambuye kuti akhululukiretu anthu ake ndi pamene timaona kusintha kwa zinthu. Pakuti Mulungu salakwitsa, koma ali wokhulupirika nthawi zonse pa anthu ake.

Komabe, potengera ndi pemphero lomwe ukupedzipempherera wekha, kapenanso anthu amtundu wako, pa miyoyo yawo, ukuyenera kuyembekeza kusintha pa anthu aja, zimene zidzaonetsera kuti mphamvu ya matemberero mwa iwo yaphwanyika tsono ndipo kuti tsono anthu ayamba kumasulidwa. Koma tsono anthu ayenera kuphunzitsidwa kukhala m'moyo wangwiro osakhalanso m'matemberero, chifukwa zinthu zina zimene zimapangitsa kuti munthu adzikhala m'moyo wa matemberero ndi mawu ochokera mkamwa mwathu, Kunene munthu wina kuti ndiwe chitsiru, kapena iwe opanda pake, kapenanso kudzitcha wekha kuti ine ndine munthu wopanda tsogolo, mawu awa amakhala amatemberero.

Ndipo pamene titsiriza kuwerenga phunziro ili, tiyeni tsono tione pemphero lili m'munsili: "Atate Mulungu wanga ndimakukondani, ndipo mu dzina lalikulu la Amuye wathu Yesu Khristu ndisowekera manja anu amphamvu kundimasula ine kumphamvu ina iliyonse ya matemberero amene anakuta moyo wanga. Atate mundikhululukire ine zolakwa zanga zonse ndinadzichita, ndi mawu ena ali onse amkamwa mwanga amene anapangitsa kuti ndikhale munthu wotembereredwa, pakuti machimo onse ndinawachita pamaso panu anandibweretsera matemberero, kaya ndinawachita mosadziwa, kaya ndinawachita ndikudziwa, amene sindinalape, sindinapepese, ndikulapa tsono (Lankhulani monga mungathere, kotengera zolakwa zanu ndipo mukatero mukhonza kupitirira kumalankhulana ndi Mulungu mwakugonja pamaso pa Mulungu), ndipo Ambuye ndikulengeza kuti zolakwa zanga ndi matemberero onse ndinawachita ndikudziwa, kapenanso ndisakudziwa, kaya polankhula amenenso anafalikira kwa anthu, zinthu zina, lolani kukhululukidwa tsopano kumene kukachitika ndi Inu. Mayamiko akhale kwa Inu Mulungu amene nthawi zonse mutipanga ife kukhala moyo wachigonjetso, (2 Akorinto chaputala cha 2:14)".

tipezeni ife